Salimo 124:1-8
Nyimbo ya Davide Yokwerera Kumzinda.
124 “Yehova akanapanda kukhala kumbali yathu,”+Isiraeli anene kuti,+
2 “Yehova akanapanda kukhala kumbali yathu,+Pamene anthu anatiukira,+
3 Akanatimeza amoyo,+Pamene mkwiyo wawo unatiyakira.+
4 Pamenepo madzi akanatikokolola,+Mtsinje wamphamvu ukanatimiza.+
5 Madzi amphamvuAkanatimiza.+
6 Yehova atamandike, chifukwa sanatipereke kwa iwo+Kuti atikhadzule ngati nyama.+
7 Moyo wathu uli ngati mbalame imene yathawa+Pamsampha wa munthu wogwiritsa ntchito nyambo.+Msamphawo wathyoka,+Ndipo ife tapulumuka.+
8 Thandizo lathu lili m’dzina la Yehova,+Wopanga kumwamba ndi dziko lapansi.”+