Salimo 131:1-3
Nyimbo ya Davide Yokwerera Kumzinda.
131 Inu Yehova, mtima wanga sunadzikweze,+Maso anga si onyada.+Sindinafune zinthu zapamwamba kwambiri,+Kapena zinthu zodabwitsa kwambiri.+
2 Ine ndadzitonthoza ndipo ndakhazika mtima wanga pansi.+Ndakhala ngati mwana amene wangosiya kumene kuyamwa, amene ali m’manja mwa mayi ake.+Ndakhala ngati mwana amene wangosiya kumene kuyamwa.+
3 Isiraeli ayembekezere Yehova,+Kuyambira tsopano mpaka kalekale.+