Salimo 138:1-8
Salimo la Davide.
138 Ndidzakutamandani ndi mtima wanga wonse.+Ndidzakuimbirani nyimbo zokutamandani pamaso pa milungu ina.+
2 Ndidzawerama nditayang’ana kukachisi wanu woyera,+Ndipo ndidzatamanda dzina lanu+Chifukwa cha kukoma mtima kwanu kosatha+ ndi choonadi chanu.+Pakuti malonjezo+ amene munawachita m’dzina lanu ndi aakulu ndithu. Koma kukwaniritsidwa kwa malonjezowo n’kwakukulu koposa.+
3 Pa tsiku limene ine ndinaitana, inu munandiyankha.+Munandilimbitsa mtima ndi kundipatsa mphamvu.+
4 Mafumu onse a padziko lapansi adzakutamandani, inu Yehova,+Pakuti adzakhala atamva mawu a pakamwa panu.
5 Ndipo iwo adzaimba za njira za Yehova,+Pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukulu.+
6 Ngakhale kuti Yehova ali pamwamba, amaona wodzichepetsa,+Koma wodzikuza samuyandikira.+
7 Ndikakhala pa masautso, inu mudzandisunga wamoyo.+Mudzatambasula dzanja lanu chifukwa cha mkwiyo wa adani anga,+Ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.+
8 Yehova adzakwaniritsa zolinga zimene ali nazo pa ine.+Inu Yehova, kukoma mtima kwanu kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+Musasiye ntchito ya manja anu.+