Salimo 143:1-12
Nyimbo ya Davide.
143 Inu Yehova, imvani pemphero langa.+Tcherani khutu pamene ndikuchonderera.+Ndiyankheni mogwirizana ndi kukhulupirika kwanu ndi chilungamo chanu.+
2 Musandiimbe mlandu ine mtumiki wanu,+Pakuti palibe aliyense wamoyo amene angakhale wolungama pamaso panu.+
3 Mdani akufunafuna moyo wanga,+Iye waupondaponda pafumbi.+Wandichititsa kukhala m’malo a mdima ngati anthu amene anafa kalekale.+
4 Mtima wanga+ walefuka,Ndipo wachita dzanzi.+
5 Ndakumbukira masiku akale.+Ndasinkhasinkha zochita zanu zonse,+Ndipo ndakhala ndikuganizira ntchito ya manja anu ndi mtima wonse.+
6 Ine ndikupemphera nditakweza manja anga kwa inu.+Moyo wanga uli ngati dziko louma limene likulakalaka kuti muthetse ludzu lake.+ [Seʹlah.]
7 Fulumirani, ndiyankheni inu Yehova.+Mphamvu zanga zatha.+Musandibisire nkhope yanu,+Chifukwa mukatero ndikhala ngati anthu amene akutsikira kudzenje la manda.+
8 M’mawa ndichititseni kumva za kukoma mtima kwanu kosatha,+Pakuti ndimadalira inu.+Ndidziwitseni njira imene ndiyenera kuyendamo,+Pakuti ndapereka moyo wanga kwa inu.+
9 Ndilanditseni kwa adani anga, inu Yehova.+Ine ndathawira kwa inu.+
10 Ndiphunzitseni kuchita chifuniro chanu,+Pakuti inu ndinu Mulungu wanga.+Mzimu wanu ndi wabwino.+Unditsogolere m’dziko la olungama.+
11 Inu Yehova, ndisungenibe wamoyo+ chifukwa cha dzina lanu.+Chotsani moyo wanga m’masautso+ monga mwa chilungamo chanu.+
12 Adani anga muwakhalitse chete monga mwa kukoma mtima kwanu kosatha.+Ndipo muwononge onse ondichitira zoipa,+Pakuti ine ndine mtumiki wanu.+