Salimo 144:1-15
Salimo la Davide.
144 Atamandike Yehova Thanthwe langa,+Amene akuphunzitsa manja anga kumenya nkhondo,+Amenenso akuphunzitsa zala zanga kumenyana ndi adani anga.
2 Iye amandisonyeza kukoma mtima kwake kosatha ndipo ndiye malo anga achitetezo,+Malo anga okwezeka ndi Wopereka chipulumutso,+Chishango+ changa ndi malo anga othawirako.+Iye amandigonjetsera mitundu ya anthu.+
3 Inu Yehova, munthu ndani kuti mumuganizire?+Kodi mwana wa munthu wochokera kufumbi+ ndani kuti mumuwerengere?
4 Munthu amafanana ndi mpweya wotuluka m’mphuno.+Masiku ake ali ngati mthunzi wongodutsa.+
5 Inu Yehova, weramitsani kumwamba kuti mutsike.+Khudzani mapiri kuti afuke utsi.+
6 Ng’animitsani mphezi kuti muwabalalitse.+Tumizani mivi yanu kuti muwasokoneze.+
7 Tambasulani manja anu kuchokera kumwamba.+Ndimasuleni ndi kundilanditsa m’madzi ambiri.+Mundilanditse m’manja mwa anthu achilendo,+
8 Anthu amene amalankhula zinthu zonama,+Amenenso dzanja lawo lamanja limachita zachinyengo.+
9 Inu Mulungu, ine ndidzakuimbirani nyimbo yatsopano.+Ndidzaimba nyimbo yokutamandani ndi choimbira cha zingwe 10.+
10 Ndidzaimbira inu amene mumapulumutsa mafumu,+Amene mumalanditsa ine Davide mtumiki wanu ku lupanga lovulaza.+
11 Ndimasuleni ndi kundilanditsa m’manja mwa anthu achilendo,+Anthu amene amalankhula zinthu zonama,+Amenenso dzanja lawo lamanja limachita zachinyengo.+
12 Anthuwo amanena kuti: “Ana athu aamuna, mu unyamata wawo, ali ngati mitengo imene yangokhwima kumene,+Ndipo ana athu aakazi ali ngati mizati yapakona yosemedwa mwaluso ya m’nyumba ya mfumu.
13 Nkhokwe zathu ndi zodzaza ndi zakudya zosiyanasiyana.+Nkhosa zathu zikuswana kukhala masauzandemasauzande. Nkhosa imodzi ikukhala masauzande 10 m’misewu.
14 Ng’ombe zathu zili ndi bere, sizikuvulala kapena kubereka ana akufa,+Ndipo palibe munthu amene akulira m’mabwalo athu.+
15 Odala ndi anthu amene zimenezi zikuwachitikira.”Ayi, koma odala ndi anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.+