Salimo 18:1-50
Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la mtumiki wa Yehova, Davide, amene anauza Yehova mawu a m’nyimbo iyi pa tsiku limene Yehova anamulanditsa m’manja mwa adani ake onse komanso m’manja mwa Sauli.+ Iye anati:
18 Ndidzakukondani inu Yehova, mphamvu yanga.+
2 Yehova ndiye thanthwe langa, malo anga achitetezo ndiponso Wopereka chipulumutso kwa ine.+Mulungu wanga ndiye thanthwe langa. Ine ndidzathawira kwa iye.+Iye ndiye chishango changa, nyanga* yanga ya chipulumutso ndiponso ndiye malo anga okwezeka achitetezo.+
3 Ndidzaitanira pa Yehova, Iye woyenera kutamandidwa,+Ndipo adzandipulumutsa kwa adani anga.+
4 Zingwe za imfa zinandikulunga,+Chikhamu cha anthu opanda pake chinali kundiopseza.+
5 Zingwe za Manda zinandizungulira.+Ndinayang’anizana ndi misampha ya imfa.+
6 Pa nthawi ya zowawa zanga ndinaitana Yehova,Ndinafuulira Mulungu wanga kuti andithandize.+Iye anamva mawu anga ali m’kachisi wake.+Pamenepo makutu ake anamva kulira kwanga kopempha thandizo.+
7 Dziko lapansi linayamba kugwedezekera uku ndi uku ndiponso kutekeseka.+Maziko a mapiri anagwedezeka,+Anagwedezekera uku ndi uku chifukwa Mulungu anakwiya.+
8 Utsi unatuluka m’mphuno mwake, ndipo moto wotuluka m’kamwa mwake unanyeketsa.+Makala onyeka anatuluka mwa iye.
9 Iye anaweramitsa kumwamba n’kutsika.+Mdima wandiweyani unali kunsi kwa mapazi ake.
10 Iye anafika atakwera pakerubi wouluka.+Mulungu anali kuuluka mwaliwiro pamapiko a cholengedwa chauzimu.*+
11 Kenako anapanga mdima kukhala malo ake obisalamo,+Panali madzi akuda ndi mtambo wakuda,Zimene zinamuzungulira ngati msasa wake.+
12 M’kuwala kochokera pamaso pake munatuluka mitambo yake,+Munatulukanso matalala ndi makala onyeka a moto.+
13 Ali kumwamba, Yehova anayamba kugunda ngati mabingu,+Wam’mwambamwamba anayamba kutulutsa mawu ake,+Anatulutsanso matalala ndi makala onyeka a moto.
14 Anayamba kuponya mivi kuti awabalalitse.+Anaponya mphezi kuti awasokoneze.+
15 Ndipo ngalande za pansi pa madzi zinaonekera,+Maziko a dziko lapansi anakhala poonekera.+Zinatero chifukwa cha kudzudzula kwanu, inu Yehova, chifukwa cha mphamvu ya mpweya wa m’mphuno mwanu.+
16 Anatambasula dzanja lake kuchokera kumwamba ndi kunditenga,+Anandivuula m’madzi akuya.+
17 Anandilanditsa kwa mdani wanga wamphamvu,+Anandilanditsa kwa odana nane chifukwa anali amphamvu kuposa ine.+
18 Adaniwo anandifikira m’tsiku la tsoka langa,+Koma Yehova anandichirikiza.+
19 Ananditenga ndi kundiika pamalo otakasuka.+Anandipulumutsa chifukwa anakondwera nane.+
20 Yehova amandipatsa mphoto mogwirizana ndi chilungamo changa.+Amandibwezera mogwirizana ndi kuyera kwa manja anga.+
21 Pakuti ndasunga njira za Yehova,+Sindinachoke kwa Mulungu wanga. Ndikanatero, ndikanachita chinthu choipa.+
22 Zigamulo zake zonse zili pamaso panga,+Ndipo malamulo ake sindidzawataya.+
23 Ndidzakhalabe wopanda cholakwa pamaso pake,+Ndipo ndidzayesetsa kupewa kuchita cholakwa.+
24 Yehova andibwezere mogwirizana ndi chilungamo changa,+Andibwezere mogwirizana ndi kuyera kwa manja anga pamaso pake.+
25 Munthu wokhulupirika, mudzamuchitira mokhulupirika.+Munthu wamphamvu wopanda cholakwa, mudzamuchitira mwachilungamo.+
26 Kwa munthu wokhalabe woyera, mudzadzisonyeza kuti ndinu woyera,+Kwa munthu wopotoka maganizo mudzadzisonyeza kuti ndinu wochenjera,+
27 Chifukwa anthu osautsika mudzawapulumutsa,+Koma anthu odzikweza mudzawatsitsa.+
28 Pakuti inu Yehova mudzandiyatsira nyale yanga,+Mulungu wanga adzandiunikira mu mdima.+
29 Pakuti ndi thandizo lanu, ndingathamangitse gulu la achifwamba.+Ndi thandizo la Mulungu wanga ndingakwere khoma.+
30 Njira ya Mulungu woona ndi yangwiro.+Mawu a Yehova ndi oyengeka bwino.+Iye ndi chishango kwa onse othawira kwa iye.+
31 Kodi pali Mulungu winanso woposa Yehova?+Kodi pali thanthwe linanso loposa Mulungu wathu?+
32 Mulungu woona Ndiye amandilimbitsa,*+Ndipo adzasalaza njira yanga.+
33 Iye adzachititsa mapazi anga kukhala aliwiro ngati a mbawala zazikazi,+Ndipo adzandiimiritsabe pamalo okwezeka kwa ine.+
34 Iye akuphunzitsa manja anga kumenya nkhondo,+Ndipo manja anga akukunga uta wamkuwa.+
35 Inu mudzandipatsa chishango chanu cha chipulumutso,+Dzanja lanu lamanja lidzandichirikiza,+Ndipo kudzichepetsa kwanu n’kumene kudzandikweza.+
36 Mudzakulitsa malo opondapo mapazi anga,+Ndipo mapazi anga sadzagwedezeka.+
37 Ndidzathamangitsa adani anga ndi kuwapeza,Ndipo sindidzabwerera kufikira nditawawononga onse.+
38 Ndidzawaphwanya zibenthuzibenthu kuti asadzukenso.+Ndidzawapondaponda ndi mapazi anga.+
39 Inu mudzandiveka mphamvu kuti ndithe kumenya nkhondo.Mudzakomola ondiukira.+
40 Koma mudzachititsa adani anga kugonja* pamaso panga,+Anthu odana nane kwambiri, ndidzawakhalitsa chete.+
41 Adzafuula kupempha thandizo, koma sipadzapezeka wowapulumutsa,+Adzafuulira Yehova, koma sadzawayankha.+
42 Ndidzawapera kukhala ngati fumbi louluzika ndi mphepo.+Ndidzawakhuthula ngati matope a mumsewu.+
43 Inu mudzandipulumutsa kwa anthu a mtundu wanga onditola zifukwa.+Mudzandiika kukhala mtsogoleri wa mitundu yonse.+Anthu amene sindikuwadziwa adzanditumikira.+
44 Anthu akangomva mphekesera chabe zokhudza ine, adzandimvera.+Alendo adzabwera kwa ine akunthunthumira.+
45 Alendo adzatha mphamvu,Ndipo adzatuluka m’malo awo achitetezo akunjenjemera.+
46 Yehova ndi wamoyo.+ Lidalitsike Thanthwe langa.+Mulungu wa chipulumutso changa akhale wokwezeka.+
47 Mulungu woona ndiye Wobwezera adani anga.+Iye amagonjetsa mitundu ya anthu ndi kuiika kunsi kwa mapazi anga.+
48 Iye amandipulumutsa kwa adani anga olusa.+Ndipo mudzandikweza pamwamba pa anthu amene amandiukira.+Mudzandilanditsa kwa munthu wachiwawa.+
49 N’chifukwa chake ndidzakutamandani, inu Yehova pakati pa mitundu.+Ndipo ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.+
50 Iye akuchita ntchito zazikulu za chipulumutso kwa mfumu yake,+Ndipo akusonyeza kukoma mtima kosatha kwa wodzozedwa wake,+kwa Davide ndi mbewu yake mpaka kalekale.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti “mapiko a mphepo.”
^ Mawu ake enieni, “amamangirira zolimba mphamvu m’chiuno mwanga.”
^ Kapena kuti “Mudzandipatsa kumbuyo kwa khosi la adani anga.”