Salimo 20:1-9
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.
20 Yehova akuyankheni pa tsiku la nsautso.+Dzina la Mulungu wa Yakobo likutetezeni.+
2 Atumize thandizo kuchokera kumalo oyera.+Akuchirikizeni ali ku Ziyoni.+
3 Akumbukire nsembe zanu zonse zimene munapereka monga mphatso.+Alandire mafuta a nsembe zanu zopsereza.+ [Seʹlah.]
4 Akupatseni zokhumba za mtima wanu,+Ndipo akwaniritse zofuna zanu.+
5 Tidzafuula mokondwera chifukwa cha chipulumutso chanu,+Tidzakweza mbendera zathu m’dzina la Mulungu wathu.+Yehova akwaniritse zopempha zanu zonse.+
6 Tsopano ndadziwa kuti Yehova amapulumutsa wodzozedwa wake.+Amamuyankha kuchokera kumwamba kwake koyera,+Amamupulumutsa ndi dzanja lake lamanja lamphamvu zopulumutsa.+
7 Ena akunena za magaleta* ndipo ena akunena za mahatchi,*+Koma ife tidzanena za dzina la Yehova Mulungu wathu.+
8 Anthu amenewo athyoka ndipo agwa,+Koma ife tanyamuka ndipo taima chilili.+
9 Inu Yehova, pulumutsani mfumu!+Tsiku limene tidzaitana, Mulungu adzatiyankha.+