Salimo 21:1-13
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.
21 Inu Yehova, mfumu ikukondwera mu mphamvu zanu.+Ndipo idzapitiriza kukondwera mu chipulumutso chanu.+
2 Mwaipatsa zokhumba za mtima wake,+Ndipo simunaimane zokhumba za pakamwa pake.+ [Seʹlah.]
3 Munaidalitsa ndi kuipatsa zinthu zabwino,+Ndipo pamutu pake munaika chisoti chachifumu chagolide woyengeka bwino.+
4 Mfumuyo inakupemphani moyo. Ndipo munaipatsadi,+Munaipatsa masiku ochuluka kuti ikhale mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+
5 Ulemerero wake ndi waukulu m’chipulumutso chanu.+Mwaipatsa ulemu ndi ulemerero.+
6 Mwaichititsa kukhala yodalitsika kwambiri mpaka muyaya.+Mwaikondweretsa ndi kuisangalatsa pamaso panu.+
7 Pakuti mfumu imakhulupirira Yehova,+Imakhulupirira kukoma mtima kosatha kwa Wam’mwambamwamba. Iyo siidzagwedezeka.+
8 Dzanja lanu lidzapeza adani anu onse.+Dzanja lanu lamanja lidzapeza odana nanu.
9 Mudzawakhalitsa ngati oponyedwa mung’anjo yamoto pa nthawi ya kuonekera kwanu.+Yehova adzawameza mu mkwiyo wake, ndipo moto udzawanyeketsa.+
10 Mudzawononga ana awo kuwachotsa padziko lapansi,+Ndipo ana awo mudzawachotsa pakati pa ana a anthu.+
11 Pakuti akuchitirani zinthu zoipa.+Alinganiza kuchita zinthu zimene sangazikwanitse.+
12 Inu mudzawachititsa kutembenuka ndi kuthawa.+Mudzachita zimenezi ndi zingwe za mauta amene mwakonzekera kuwalasa nawo pankhope.+
13 Inu Yehova, mukhale wokwezeka mu mphamvu zanu.+Tidzaimba ndi kutamanda mphamvu zanu.+