Salimo 27:1-14
Salimo la Davide.
27 Yehova ndiye kuwala+ kwanga ndi chipulumutso changa.+Ndingaopenso ndani?+Yehova ndiye malo a chitetezo cha moyo wanga.+Ndingachitenso mantha ndi ndani?+
2 Anthu ochita zoipa atandiyandikira kuti adye mnofu wanga,+Popeza kuti iwo ndi ondiukira komanso adani anga,+Anapunthwa ndi kugwa.+
3 Ngakhale gulu lankhondo litamanga msasa kuti lindiukire,+Mtima wanga sudzachita mantha.+Ngakhale nkhondo yolimbana ndi ine itayambika,+Pameneponso ndidzadalira Mulungu.+
4 Chinthu chimodzi chimene ndapempha kwa Yehova,+Chimenecho ndi chimene ndimachikhumba,+N’chakuti, ndikhale m’nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga,+Kuti ndione ubwino wa Yehova,+Komanso kuti ndiyang’ane kachisi wake moyamikira.+
5 Pakuti pa tsiku la tsoka, iye adzandibisa m’malo ake otetezeka.+Adzandibisa m’malo obisika m’hema wake.+Adzandiika pamwamba, pathanthwe.+
6 Pamenepo mutu wanga udzakwezeka pamwamba pa adani onse ondizungulira.+Ndipo ndidzapereka nsembe za kufuula mokondwera pahema wake.+Ndidzamuimbira nyimbo, ndithu ndidzaimba nyimbo zotamanda Yehova.+
7 Inu Yehova, imvani mawu anga pamene ndikuitana.+Ndikomereni mtima ndi kundiyankha.+
8 Mtima wanga wanena lamulo lanu lakuti: “Ndifunefuneni anthu inu.”+Ndidzakufunafunani, inu Yehova.+
9 Musandibisire nkhope yanu.+Musabweze mtumiki wanu mutakwiya.+Inu mukhale mthandizi wanga.+Musanditaye ndi kundisiya, inu Mulungu wa chipulumutso changa.+
10 Ngakhale bambo anga ndi mayi anga atandisiya,+Yehova adzanditenga.+
11 Ndilangizeni, inu Yehova, kuti ndiyende m’njira yanu.+Nditsogolereni m’njira yowongoka kuti nditetezeke kwa adani anga.
12 Musandipereke kwa adani anga.+Pakuti mboni zonama zandiukira,+Chimodzimodzinso munthu wachiwawa.+
13 Ngati ndikanakhala wopanda chikhulupiriro poona ubwino wa Yehova m’dziko la anthu amoyo, ndikanataya chiyembekezo.+
14 Yembekezera Yehova.+ Limba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu.+Yembekezera Yehova.+