Salimo 3:1-8
Nyimbo ya Davide pamene anali kuthawa mwana wake Abisalomu.+
3 Inu Yehova, n’chifukwa chiyani adani anga achuluka chotere?+N’chifukwa chiyani anthu ondiukira achuluka?+
2 Ponena za moyo wanga, ambiri akuti:“Mulungu sam’pulumutsa ameneyu.”+ [Seʹlah.*]
3 Koma inu Yehova ndinu chishango changa,+Ulemerero wanga+ ndiponso Wonditukula mutu.+
4 Ndidzafuulira Yehova mokweza,Ndipo iye adzandiyankha m’phiri lake loyera.+ [Seʹlah.]
5 Koma ine ndidzagona pansi ndi kupeza tulo.Ndidzadzuka ndithu, pakuti Yehova amandithandiza.+
6 Sindidzaopa anthu masauzande makumimakumiAmene andiukira ndi kundizungulira.+
7 Nyamukani,+ inu Yehova! Ndipulumutseni+ inu Mulungu wanga!+Pakuti mudzakantha adani anga onse pachibwano.+Mano a anthu oipa mudzawaphwanyaphwanya.+
8 Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.+Madalitso anu ali pa anthu anu.+ [Seʹlah.]
Mawu a M'munsi
^ “Seʹlah” ndi mawu achiheberi amene anali kuwagwiritsa ntchito polemba nyimbo kapena ndakatulo. Tanthauzo lake lenileni silikudziwika.