Salimo 32:1-11
Salimo la Davide. Masikili.*
32 Wodala ndi munthu amene wakhululukidwa zolakwa zake, amene machimo ake aphimbidwa.+
2 Wodala ndi munthu amene Yehova sanamusungire cholakwa chake,+Amene alibe mtima wachinyengo.+
3 Pamene ndinakhala chete osaulula machimo anga, mafupa anga anafooka, chifukwa tsiku lonse ndinali kuvutika mumtima mwanga.+
4 Pakuti dzanja lanu linali kundilemera usana ndi usiku.+Mphamvu zanga zinauma ngati madzi m’nyengo yotentha ya chilimwe.+ [Seʹlah.]
5 Pamapeto pake ndinaulula tchimo langa kwa inu, ndipo sindinabise cholakwa changa.+Ndinati: “Ndidzaulula kwa Yehova machimo anga.”+Ndipo inu munandikhululukira zolakwa zanga ndi machimo anga.+ [Seʹlah.]
6 Pa chifukwa chimenechi, aliyense wokhulupirika adzapemphera kwa inu,+Pa nthawi imene inu mungapezeke.+Ndipo madzi ambiri osefukira sadzamukhudza ngakhale pang’ono.+
7 Ndinu malo anga obisalamo, mudzanditeteza ku masautso.+Mudzachititsa kuti chisangalalo chindizungulire pamene mukundipulumutsa.+ [Seʹlah.]
8 Inu munati: “Ndidzakupatsa nzeru ndi kukulangiza njira yoti uyendemo.+Ndidzakupatsa malangizo ndi kukuyang’anira.+
9 Anthu inu, musakhale ngati hatchi kapena nyulu* yosazindikira,+Imene munthu amachita kuimanga chingwe chapakamwa ndi chapamutu kuti athetse kupulupudza kwake,+Ndi kuti aiyandikire.”+
10 Zopweteka za woipa ndi zambiri.Koma wokhulupirira Yehova+ amazunguliridwa ndi kukoma mtima kosatha.+
11 Inu olungama, kondwerani chifukwa cha zimene Yehova wachita ndipo sangalalani.+Fuulani ndi chisangalalo inu nonse owongoka mtima.+
Mawu a M'munsi
^ “Masikili” ndi mawu achiheberi amene tanthauzo lake silikudziwika. N’kutheka kuti amatanthauza “ndakatulo imene munthu amanena posinkhasinkha.”