Salimo 36:1-12
Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide, mtumiki wa Yehova.
36 Uchimo ukulankhula mumtima mwa munthu woipa.+Maso ake saona chifukwa choopera Mulungu.+
2 Pakuti amadzinyenga yekha,+Ndipo sazindikira cholakwa chake ndi kudana nacho.+
3 Mawu a pakamwa pake ndi opweteka ndi achinyengo.+Wasiya kugwiritsa ntchito nzeru zomuthandiza kuchita zinthu zabwino.+
4 Ali pabedi lake amakonza chiwembu kuti apweteke anzake.+Amaima panjira yoipa.+Sapewa kuchita zinthu zoipa.+
5 Inu Yehova, kukoma mtima kwanu kosatha kuli kumwamba.+Kukhulupirika kwanu kwafika m’mitambo.+
6 Inu Mulungu, chilungamo chanu chili ngati mapiri anu.+Chiweruzo chanu ndi chozama kwambiri ngati madzi akuya.+Inu Yehova, mumapulumutsa munthu ndiponso nyama.+
7 Inu Mulungu, kukoma mtima kwanu kosatha ndi kwamtengo wapatali!+Ndipo ana a anthu amabisala mu mthunzi wa mapiko anu.+
8 Amadya ndi kukhuta chakudya chonona m’nyumba mwanu.+Ndipo mumawamwetsa mumtsinje wa zosangalatsa zanu zambiri.+
9 Pakuti inu ndinu kasupe wa moyo.+Chifukwa cha kuwala kochokera kwa inu, tikuona kuwala.+
10 Pitirizani kusonyeza kukoma mtima kwanu kosatha kwa anthu okudziwani,+Ndiponso chilungamo chanu kwa anthu owongoka mtima.+
11 Musalole kuti phazi la anthu odzikweza lindipondereze.+Ndipo musalole dzanja la anthu oipa kundipitikitsa kuti ndikhale wothawathawa.+
12 Onani, ochita zinthu zopweteka anzawo agwa.+Awakanikizira pansi ndipo sakuthanso kudzuka.+