Salimo 38:1-22
Nyimbo ya Davide ya chikumbutso.
38 Inu Yehova, musandidzudzule mutakwiya,+Kapena kundilanga mutapsa mtima.+
2 Pakuti mivi yanu yandilasa kwambiri,+Ndipo dzanja lanu likundilemera.+
3 Palibe pabwino m’thupi langa chifukwa cha chidzudzulo chanu.+Ndipo m’mafupa anga mulibe mtendere chifukwa cha tchimo langa.+
4 Pakuti zolakwa zanga zakwera kupitirira mutu wanga.+Zandilemera kwambiri ngati katundu wolemera.+
5 Zilonda zanga zanunkha ndi kunyeka,Chifukwa cha kupusa kwanga.+
6 Ndasokonezeka ndipo ndawerama kwambiri chifukwa cha chisoni changa.+Ndayenda uku ndi uku tsiku lonse ndili wachisoni.+
7 M’chiuno mwanga mukutentha kwambiri,Ndipo palibe paliponse pabwino m’thupi langa.+
8 Ndalefuka ndipo ndaponderezeka kwambiri.Ndikulira mofuula chifukwa cha kuvutika kwa mtima wanga.+
9 Inu Yehova, zokhumba zanga zonse zili pamaso panu,Kudandaula kwanga sikunabisike kwa inu.+
10 Mtima wanga ukugunda kwambiri, ndipo mphamvu zanga zatha,Maso anga achita mdima.+
11 Anthu amene anali kundikonda ndiponso anzanga aima patali chifukwa cha kuvutika kwanga,+Ndipo mabwenzi anga apamtima anditalikira.+
12 Anthu amene akufuna kundiwononga anditchera misampha,+Amene akufuna kundivulaza akulankhula motsutsana nane,+Ndipo amakhala akukonza zachinyengo tsiku lonse.+
13 Koma ine ndakhala ngati munthu wogontha, sindikumvetsera,+Ndakhala ngati munthu wosalankhula, sindikutsegula pakamwa.+
14 Ndakhala ngati munthu wosamva,Sindikulankhula zotsutsana nawo.
15 Pakuti ine ndikuyembekezera inu Yehova.+Inu Yehova Mulungu wanga, mudzandiyankha.+
16 Ine ndinati: “Ngati simundiyankha adani anga adzasangalala chifukwa cha kusautsika kwanga.+Phazi langa likaterereka,+ iwo adzadzikweza pamaso panga.”+
17 Ndinali pafupi kupunthwa,+Ndipo ndinali kumva ululu nthawi zonse.+
18 Pakuti ndinali kulankhula za cholakwa changa.+Ndipo ndinali kudera nkhawa za tchimo langa.+
19 Adani anga anali amphamvu kwambiri,+Ndipo odana nane popanda chifukwa anachuluka.+
20 Iwo anali kundibwezera choipa m’malo mwa chabwino,+Ndikamayesetsa kuchita chabwino anali kunditsutsa.+
21 Inu Yehova, musandisiye.Inu Mulungu wanga, musakhale kutali ndi ine.+
22 Fulumirani kundithandiza,+Inu Yehova, chipulumutso changa.+