Salimo 39:1-13

Kwa wotsogolera nyimbo pa Yedutuni.*+ Nyimbo ya Davide. 39  Ine ndinati: “Ndidzatchinjiriza njira zanga,+Kuti ndisachimwe ndi lilime langa.+Ndidzamanga pakamwa panga kuti patetezeke,+Nthawi zonse pamene woipa ali pamaso panga.”+   Ndinakhala chete osalankhula kanthu.+Ndinakhala phee osanena ngakhale zinthu zabwino,+Ndipo ndinanyalanyaza ululu wanga.   Mumtima mwanga munatentha moto.+Pamene ndinali kuusa moyo, moto unali kuyakabe.Choncho ndinati:   “Inu Yehova, ndidziwitseni za kufulumira kwa chimaliziro changa,+Ndiponso kuti masiku anga ndi ochepa motani,+Kuti ndidziwe kufupika kwa moyo wanga.+   Taonani! Mwachepetsa masiku anga.+Ndipo nthawi ya moyo wanga si kanthu pamaso panu.+Ndithudi, munthu aliyense ngakhale atakhala wamphamvu bwanji, sali kanthu koma ali ngati mpweya wotuluka m’mphuno.+ [Seʹlah.]   Zoonadi, munthu amayenda ngati chithunzithunzi.+Ndithudi, anthu amapokosera pachabe.+Munthu amaunjika zinthu ndipo sadziwa amene adzazitute.+   Nanga tsopano, inu Yehova, ine ndikuyembekezera chiyani?Chiyembekezo changa chili mwa inu.+   Ndilanditseni ku zolakwa zanga zonse.+Musalole kuti munthu wopusa azinditonza.+   Ndinakhala chete.+ Sindinatsegule pakamwa panga,+Pakuti inu munachitapo kanthu.+ 10  Ndichotsereni mliri umene mwandigwetsera.+Ine ndatha chifukwa cha ukali wa dzanja lanu.+ 11  Mwa kudzudzula cholakwa, mwawongolera munthu,+Ndipo mwawononga zinthu zake zamtengo wapatali ngati mmene njenjete*+ imachitira.Ndithudi, munthu aliyense ali ngati mpweya.+ [Seʹlah.] 12  Imvani pemphero langa, inu Yehova,Ndipo tcherani khutu pamene ndikufuula kupempha thandizo.+Musandinyalanyaze pamene ndikugwetsa misozi.+Pakuti ndine mlendo wanu,+Mlendo wokhala nanu monga anachitira makolo anga onse.+ 13  Musandiyang’ane mutakwiya, kuti ndikhalenso wosangalala+Ndisanamwalire ndi kuiwalika.”+

Mawu a M'munsi

“Yedutuni” ndi mawu achiheberi amene tanthauzo lake silikudziwika.
Mawu achiheberi amene tawamasulira kuti “njenjete” amatanthauza mtundu wa kachilombo kotchedwa kadziwotche kooneka ngati gulugufe, kamene kamadya zovala ngati mmene njenjete imachitira.