Salimo 59:1-17

Kwa wotsogolera nyimbo. “Musandiwononge.” Salimo la Davide. Mikitamu.* Pa nthawi imene Sauli anatumiza anthu, ndipo anali kudikirira nyumba yake kuti amuphe.+ 59  Inu Mulungu wanga, ndilanditseni kwa adani anga.+Nditetezeni kwa anthu amene akundiukira.+   Ndilanditseni kwa anthu ochita zopweteka anzawo,+Ndipo ndipulumutseni kwa anthu amene ali ndi mlandu wa magazi.   Pakuti, taonani! Iwo akundidikirira kuti awononge moyo wanga.+Inu Yehova, anthu amphamvu akundiukira,+Ngakhale kuti ine sindinapanduke kapena kuchita tchimo lililonse.+   Iwo akuthamanga ndi kukonzekera kundiukira, ngakhale kuti sindinalakwe chilichonse.+Nyamukani pamene ine ndikuitana kuti muone zimene zikundichitikira.+   Inu Yehova, Mulungu wa makamu, ndinu Mulungu wa Isiraeli.+Nyamukani ndi kuweruza mitundu yonse ya anthu.+Musakomere mtima aliyense woipa ndi wachiwembu.+ [Seʹlah.]   Madzulo amabweranso.+Ndipo amauwa ngati agalu+ ndi kuzungulira mzinda wonse.+   Taonani! Amabwetuka ndi pakamwa pawo.+Milomo yawo ili ngati malupanga,+Pakuti iwo amati: “Ndani akumvetsera?”+   Koma inu Yehova, mudzawaseka.+Mudzanyoza mitundu yonse ya anthu.+   Inu Mphamvu yanga, ndidzayang’anabe kwa inu.+Pakuti Mulungu ndiye malo anga okwezeka ndiponso achitetezo.+ 10  Mulungu amene wandisonyeza kukoma mtima kosatha ndidzaonana naye maso ndi maso.+Mulungu adzachititsa kuti ndione adani anga, adaniwo atagonja.+ 11  Musawaphe, kuti anthu a mtundu wanga angaiwale.+Ndi mphamvu zanu zochuluka achititseni kuyendayenda,+Ndipo agwetseni, inu Yehova, chishango chathu,+ 12  Chifukwa cha tchimo la pakamwa pawo, ndi mawu a pamilomo yawo.+Agwidwe chifukwa cha kunyada kwawo,+Chifukwa cha kutukwana ndi chinyengo zimene amachita mobwerezabwereza. 13  Afafanizeni mu mkwiyo wanu.+Afafanizeni kuti asakhaleponso.Ndipo adziwe kuti Mulungu akulamulira Yakobo mpaka kumalekezero a dziko lonse lapansi.+ [Seʹlah.] 14  Asiyeni abwerenso madzulo.Asiyeni auwe ngati agalu ndipo azungulire mzinda wonse.+ 15  Asiyeni amenewo ayendeyende kufunafuna chakudya.+Asakhute ndipo usiku asowe malo ogona.+ 16  Koma ine, ndidzaimba za mphamvu yanu,+M’mawa ndidzanena mosangalala za kukoma mtima kwanu kosatha.+Pakuti inu mwakhala malo anga okwezeka ndiponso achitetezo,+Ndiponso malo anga othawirako pa nthawi ya masautso.+ 17  Inu Mphamvu yanga, ine ndidzaimba nyimbo zokutamandani,+Pakuti Mulungu ndiye malo anga okwezeka ndiponso achitetezo, Mulungu wandisonyeza kukoma mtima kosatha.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Sl 16:Kamutu.