Salimo 6:1-10
Kwa wotsogolera nyimbo: Nyimboyi iimbidwe chapansipansi* ndi zoimbira za zingwe.+ Nyimbo ya Davide.
6 Inu Yehova, musandidzudzule mutakwiya.+Musandiwongolere mutapsa mtima.+
2 Ndikomereni mtima, inu Yehova, chifukwa ndikulefuka.+Ndichiritseni,+ inu Yehova, chifukwa mafupa anga agwedezeka.
3 Moyo wanga wasokonezeka kwambiri.+Kodi inu Yehova, mudzadikira kufikira liti?+
4 Bwererani+ mudzapulumutse moyo wanga, inu Yehova.+Ndipulumutseni chifukwa cha kukoma mtima kwanu kosatha.+
5 Pakuti akufa satchula za inu.+Kodi ndani angatamande inu ali m’Manda?*+
6 Ndalefuka chifukwa cha kuusa moyo* kwanga.+Usiku wonse ndimanyowetsa bedi langa.+Ndimakhathamitsa bedi langa ndi misozi.+
7 Maso anga achita mdima chifukwa cha chisoni changa.+Maso anga akalamba chifukwa cha anthu onse ondichitira zoipa.+
8 Ndichokereni pamaso panga inu nonse ochita zopweteka ena,+Chifukwa Yehova adzamva ndithu mawu a kulira kwanga.+
9 Yehova adzamva ndithu pempho langa loti andikomere mtima.+Yehova adzalandira pemphero langa.+
10 Adani anga onse adzachita manyazi kwambiri+ ndipo adzasokonezeka.Adzabwerera, ndipo nthawi yomweyo adzachita manyazi.+
Mawu a M'munsi
^ N’kutheka kuti mawu amene tawamasulira kuti “chapansipansi” akutanthauza kuti anali kuimba nyimbo imeneyi motsitsa kapena mwabesi.
^ Onani Zakumapeto 5.
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.