Salimo 72:1-20
Salimo lonena za Solomo.
72 Inu Mulungu, dziwitsani mfumu za zigamulo zanu,+Ndipo dziwitsani mwana wa mfumu za chilungamo chanu.+
2 Aweruzire anthu milandu mwachilungamo,+Ndipo aweruze milandu ya osautsika ndi ziweruzo zolungama.+
3 Mapiri atenge mtendere ndi kupita nawo kwa anthu,+Komanso zitunda zitenge mtendere wopezeka mwachilungamo.
4 Aweruze osautsika pakati pa anthu,+Apulumutse ana a anthu osauka,Ndipo aphwanye wobera anzake mwachinyengo.
5 Iwo adzakuopani nthawi zonse pamene dzuwa likuwala,+Adzakuopani ku mibadwomibadwo pamene mwezi uli kuthambo.+
6 Adzatsika ngati mvula pa udzu umene wadulidwa,+Ngati mvula yambiri yamvumbi imene imanyowetsa kwambiri nthaka.+
7 M’masiku ake, wolungama adzaphuka,+Ndipo padzakhala mtendere wochuluka kwa nthawi yonse pamene mwezi udzakhalepo.+
8 Ndipo adzakhala ndi anthu omugonjera kuchokera kunyanja kukafika kunyanja,+Komanso kuchokera ku Mtsinje*+ kukafika kumalekezero a dziko lapansi.+
9 Anthu okhala m’madera opanda madzi adzagwada pamaso pake,+Ndipo adani ake adzabwira fumbi.+
10 Mafumu a ku Tarisi ndi m’zilumba+Adzapereka msonkho.+Mafumu a ku Sheba ndi SebaAdzapereka mphatso.+
11 Mafumu onse adzamugwadira ndi kumuweramira.+Ndipo mitundu yonse ya anthu idzamutumikira.+
12 Pakuti adzalanditsa wosauka amene akufuula popempha thandizo,+Komanso wosautsika ndi aliyense wopanda womuthandiza.+
13 Adzamvera chisoni munthu wonyozeka ndi wosauka,+Ndipo adzapulumutsa miyoyo ya anthu osauka.+
14 Adzawombola miyoyo yawo ku chipsinjo ndi chiwawa,Ndipo adzaona magazi awo kukhala amtengo wapatali.+
15 Iye akhale ndi moyo wautali,+ ndipo apatsidwe wina mwa golide wa ku Sheba.+Nthawi zonse anthu azimupempherera.Adalitsike tsiku lililonse.+
16 Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri.+Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka.+Zokolola za mfumu zidzachuluka ngati mitengo ya ku Lebanoni,+Ndipo anthu ochokera mumzinda adzaphuka ngati udzu wa panthaka.+
17 Dzina lake likhalebe mpaka kalekale.+Nthawi zonse pamene dzuwa latuluka, dzina lake lizitchuka,Ndipo kudzera mwa iye, anthu apeze madalitso.*+Mitundu yonse ya anthu imutche wodala.+
18 Adalitsike Yehova Mulungu, Mulungu wa Isiraeli,+Iye yekha amene akuchita ntchito zodabwitsa.+
19 Lidalitsike dzina lake laulemerero mpaka kalekale,+Ndipo ulemerero wake udzaze dziko lonse lapansi.+Ame! Ame!*
20 Mapemphero a Davide mwana wa Jese,+ athera pamenepa.
Mawu a M'munsi
^ Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
^ Kapena kuti “adzadzidalitsa okha,” kusonyeza kuti akufunika kuchitapo kanthu kuti alandire madalitso amenewo.
^ Kapena kuti “Zikhale momwemo! Zikhale momwemo!”