Salimo 73:1-28
Nyimbo ya Asafu.+
73 Mulungu ndi wabwinodi kwa Isiraeli, kwa anthu oyera mtima.+
2 Koma ine phazi langa linangotsala pang’ono kupatuka,+Mapazi anga anangotsala pang’ono kuterereka.+
3 Pakuti ndinachitira nsanje anthu odzitukumula,+Ndikamaona mtendere wa anthu oipa.+
4 Pakuti samva zowawa za imfa.+Ndipo mimba zawo ndi zazikulu chifukwa cha kunenepa.+
5 Iwo sakumana ndi mavuto amene anthu onse amakumana nawo,+Ndipo sakumana ndi masoka mofanana ndi anthu ena onse.+
6 Choncho kudzikuza kuli ngati mkanda m’khosi mwawo,+Ndipo avala chiwawa ngati malaya.+
7 Diso lawo latuzuka chifukwa cha kunenepa.+Achita zambiri kuposa zolingalira za mtima wawo.+
8 Iwo amanyodola ndi kulankhula zinthu zoipa.+Amalankhula za chinyengo chawo modzikweza.+
9 Kudzikweza kwawo kwafika kumwamba,+Akuyendayenda padziko lapansi ndipo lilime lawo likunena zilizonse zimene akufuna.+
10 Choncho woipa amatengera anthu a Mulungu kumalo omwewo,Ndipo amamwa madzi m’kapu yodzaza bwino.
11 Iwo anena kuti: “Mulungu angadziwe bwanji?+Kodi Wam’mwambamwamba akudziwa zimenezi?”+
12 Onani! Awa ndi anthu oipa, amene akukhala mosatekeseka mpaka kalekale.+Iwo achulukitsa chuma chawo.+
13 Ndithudi, ndayeretsa mtima wanga pachabe,+Ndipo ndasamba m’manja mwanga pachabe posonyeza kuti ndine wopanda cholakwa.+
14 Ndinali kukumana ndi masoka tsiku lililonse,+Ndipo m’mawa uliwonse ndinali kudzudzulidwa.+
15 Ngati ndikananena kuti: “Ndidzalankhula za zinthu zimenezi,”Pamenepo ndikanachitira chinyengoM’badwo wa ana anu aamuna.+
16 Ndipo ndinali kuganizira nkhani imeneyi kuti ndiimvetse.+Zinali zopweteka kwa ine,
17 Kufikira pamene ndinalowa m’malo opatulika aulemerero a Mulungu.+Ndinafuna kudziwa za tsogolo lawo.+
18 Ndithudi, mwawaimika pamalo oterera.+Mwawagwetsa kuti awonongeke.+
19 Haa! M’kanthawi kochepa, iwo akhala chinthu chodabwitsa.+Afika pamapeto awo ndipo atha chifukwa cha masoka owagwera modzidzimutsa!
20 Inu Yehova, anthu amenewa ali ngati maloto amene aiwalika podzuka.+Choncho pamene mukuimirira mudzawakana mochititsa manyazi.+
21 Pakuti mtima unandipweteka+Ndipo ndinamva ululu mu impso zanga.+
22 Ndinakhala wopanda nzeru ndipo sindinadziwe kanthu.+Ndinakhala ngati nyama yakuthengo pamaso panu.+
23 Koma ine ndili ndi inu nthawi zonse.+Mwandigwira dzanja langa lamanja.+
24 Mudzanditsogolera ndi malangizo anu,+Ndipo pambuyo pake mudzanditenga ndi kundipatsa ulemerero.+
25 Winanso ndani kumwambako amene ali kumbali yanga?+Palibe wina wondisangalatsa padziko lapansi koma inu nokha.+
26 Thupi langa ndi mtima wanga zalefuka.+Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga ndiponso cholowa changa mpaka kalekale.+
27 Pakuti onse okhala kutali ndi inu adzatheratu.+Mudzawononga ndithu aliyense wochita chigololo mwa kukusiyani.+
28 Koma kwa ine kuyandikira kwa Mulungu ndi chinthu chabwino.+Yehova Ambuye Wamkulu Koposa ndiye pothawirapo panga,+Kuti ndilengeze za ntchito zanu zonse.+