Salimo 75:1-10

Kwa wotsogolera nyimbo. “Musandiwononge.” Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+ 75  Timakuyamikani, inu Mulungu, timakuyamikani,+Ndipo dzina lanu lili pafupi ndi ife.+Anthu ayenera kulengeza ntchito zanu zodabwitsa.+   Mulungu akuti:* “Ndinasankha nthawi yoikidwiratu,+Ndipo ndinayamba kuweruza mwachilungamo.+   Dziko lapansi ndi onse okhala mmenemo anayamba kusungunuka chifukwa cha mantha,+Ndine amene ndinakonzanso zipilala zake.”+ [Seʹlah.]   Anthu opusa ndinawauza kuti: “Musakhale opusa,”+Ndipo oipa ndinawauza kuti: “Musakweze nyanga.*+   Musakweze nyanga yanu pamwamba.Musalankhule modzikuza.+   Pakuti kukwezeka kwa munthu sikuchokera kum’mawa,Kumadzulo kapena kum’mwera.   Mulungu ndiye woweruza.+Amatsitsa wina ndi kukweza wina.+   M’dzanja la Yehova muli kapu.+Kapuyo yadzaza ndi vinyo wosakaniza ndi zokometsera ndipo akuchita thovu.Ndithudi, iye adzatsanula vinyo yense amene ali m’kapuyo kuphatikizapo nsenga zake.Anthu onse oipa padziko lapansi adzamwa ndi kugugudiza nsengazo.”+   Koma ine ndidzasimba zimenezi mpaka kalekale.Ndidzaimba nyimbo zotamanda Mulungu wa Yakobo.+ 10  Mulungu akuti:* “Ndidzadula nyanga zonse za anthu oipa.”+Koma nyanga za munthu wolungama zidzakwezedwa.+

Mawu a M'munsi

M’Malemba achiheberi mulibe mawu akuti “Mulungu akuti,” koma aikidwapo pofuna kusonyeza amene akulankhula m’mavesi 2 ndi 3.
Onani mawu a m’munsi pa 1Sa 2:1.
Onani mawu a m’munsi pa vesi 2.