Salimo 87:1-7
Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.
87 Maziko a mzinda wa Mulungu ali m’mapiri opatulika.+
2 Yehova amakonda kwambiri zipata za Ziyoni+Kusiyana ndi mahema onse a Yakobo.+
3 Iwe mzinda wa Mulungu woona, anthu akunena za ulemerero wako.+ [Seʹlah.]
4 Ine ndidzatchula Rahabi*+ ndi Babulo+ monga ena mwa amene akundidziwa.Ponena za Filisitiya,+ Turo ndi Kusi ine ndidzati:“Amenewa anabadwira m’Ziyoni.”+
5 Ponena za Ziyoni anthu adzati:“Aliyense anabadwira mmenemo.”+Ndipo Wam’mwambamwamba+ adzakhazikitsa mzinda umenewo.+
6 Powerenga mitundu ya anthu, Yehova adzalengeza kuti:+“Amenewa anabadwira m’Ziyoni.”+ [Seʹlah.]
7 Kudzakhalanso oimba komanso ovina gule wovina mozungulira amene adzati:+“Akasupe anga onse ali mwa iwe.”+
Mawu a M'munsi
^ Zikuoneka kuti dzina lakuti “Rahabi” likuimira dziko la Iguputo.