Salimo 88:1-18
Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora. Kwa wotsogolera nyimbo pa Mahalati.* Iimbidwe molandizana. Masikili* ya Hemani+ wa m’banja la Zera.
88 Inu Yehova, Mulungu wa chipulumutso changa,+Masana ndimafuula kwa inu,+Usikunso ndimafuula pamaso panu.+
2 Pemphero langa lidzafika kwa inu.+Tcherani khutu lanu kuti mumve kuchonderera kwanga.+
3 Pakuti ine ndakumana ndi masoka ochuluka,+Ndipo moyo wanga wayandikira ku Manda.+
4 Anandiika m’gulu la anthu otsikira kudzenje.+Ndakhala ngati mwamuna wanyonga zake koma wopanda mphamvu.+
5 Ndakhala womasuka ngati anthu akufa,+Ngati anthu ophedwa amene agona m’manda,+Anthu amene simukuwakumbukiransoKomanso amene sakulandira thandizo kuchokera m’manja mwanu.+
6 Mwandiika m’dzenje lakuya kwambiri,M’malo a mdima, m’phompho lalikulu.+
7 Mkwiyo wanu wagwera pa ine,+Ndipo mwandisautsa ndi mafunde anu onse amphamvu.+ [Seʹlah.]
8 Anzanga mwawaika kutali ndi ine.+Mwandisandutsa chinthu chonyansa kwa iwo.+Ndatsekerezedwa ndipo sindingathenso kuchoka.+
9 Diso langa lafooka chifukwa cha kusautsika kwanga.+Ndaitana inu Yehova tsiku lonse.+Ndapemphera kwa inu nditakweza manja anga.+
10 Kodi anthu akufa mudzawachitira zodabwitsa?+Kapena kodi anthu akufa, anthu amene sangachite kanthu, adzauka?+Kodi adzakutamandani?+ [Seʹlah.]
11 Kodi adzalengeza za kukoma mtima kwanu kosatha m’manda?Kodi adzalengeza za kukhulupirika kwanu m’malo a chiwonongeko?+
12 Kodi zodabwitsa zimene inu mukuchita zidzadziwika mu mdima?+Kapena kodi chilungamo chanu chidzadziwika m’dziko la anthu oiwalika?+
13 Koma ine ndafuulira inu Yehova kupempha thandizo,+Ndipo m’mawa mapemphero anga amafika kwa inu nthawi zonse.+
14 Inu Yehova, n’chifukwa chiyani mukunditaya?+N’chifukwa chiyani mukundibisira nkhope yanu?+
15 Kuyambira pa unyamata wanga ndakhala ndikusautsika komanso kutsala pang’ono kufa.+Ndapirira kwambiri zinthu zoopsa zochokera kwa inu.+
16 Mafunde a mkwiyo wanu woyaka moto andimiza.+Zinthu zochititsa mantha zochokera kwa inu zandisowetsa chonena.+
17 Zandizungulira ngati madzi tsiku lonse.+Zandimiza pa nthawi imodzi.
18 Bwenzi langa ndi mnzanga mwawaika kutali kwambiri.+Malo a mdima ndiwo anzanga apamtima.+