Salimo 92:1-15
Nyimbo ndi Salimo la pa tsiku la sabata.
92 Ndi bwino kuyamika inu Yehova,+Ndi kuimba nyimbo zotamanda dzina lanu, inu Wam’mwambamwamba.+
2 Ndi bwino kunena za kukoma mtima kwanu kosatha m’mawa,+Ndi za kukhulupirika kwanu usiku,+
3 Ndipo ndidzatero pogwiritsa ntchito choimbira cha zingwe 10 ndi choimbira cha zingwe zitatu.+Ndidzaimba nyimbo yomveka bwino ndi zeze.+
4 Pakuti mwandichititsa kusangalala, inu Yehova, chifukwa cha zochita zanu.Ndimafuula mosangalala chifukwa cha ntchito ya manja anu.+
5 Ntchito zanu ndi zazikuludi inu Yehova!+Maganizo anu ndi ozama kwambiri.+
6 Munthu wopanda nzeru sangadziwe zimenezi,+Ndipo munthu wopusa sangazimvetse.+
7 Anthu oipa akamaphuka ngati msipu,+Ndipo anthu onse ochita zopweteka anzawo akamaphuka ngati maluwa,Amatero kuti awonongeke kwamuyaya.+
8 Koma inu Yehova, ndinu wokwezeka mpaka kalekale.+
9 Pakuti taonani adani anu, inu Yehova!+Adani anu onse adzatha!+Anthu onse ochita zopweteka anzawo adzamwazikana.+
10 Koma inu mudzakweza nyanga* yanga ngati nyanga ya ng’ombe yam’tchire yamphongo.*+Ndidzadzola mafuta abwino.+
11 Diso langa lidzayang’ana adani anga atagonja,+Makutu anga adzamva za anthu ondiukira, anthu ochita zoipa.
12 Wolungama adzakula ngati mtengo wa kanjedza,+Ndipo adzakula kwambiri ngati mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni.+
13 Anthu obzalidwa m’nyumba ya Yehova,+M’mabwalo a Mulungu wathu,+ adzakula mosangalala.
14 Zinthu zidzapitiriza kuwayendera bwino ngakhale atachita imvi,+Adzakhalabe onenepa ndi athanzi,+
15 Kuti alengeze kuti Yehova ndi wolungama.+Iye ndi Thanthwe langa,+ ndipo sachita zosalungama.+