Salimo 97:1-12
97 Yehova wakhala mfumu!+ Dziko lapansi likondwere,+Ndipo zilumba zambiri zisangalale.+
2 Mitambo ndi mdima wandiweyani zamuzungulira.+Chilungamo ndi chiweruzo ndizo malo okhazikika a mpando wake wachifumu.+
3 Patsogolo pake pakuyaka moto,+Ndipo ukupsereza adani ake onse omuzungulira.+
4 Mphezi zake zinawalitsa dziko lapansi.+Dziko linaona ndipo linachita mantha kwambiri.+
5 Mapiri anasungunuka ngati phula chifukwa cha Yehova,+Chifukwa cha Ambuye wa dziko lonse lapansi.+
6 Kumwamba kwalengeza za chilungamo chake,+Ndipo mitundu yonse ya anthu yaona ulemerero wake.+
7 Onse amene akupembedza chifaniziro chilichonse achite manyazi.+Amene amadzitama chifukwa cha milungu yopanda pake achite manyazi.+Muweramireni, inu milungu yonse.+
8 Ziyoni anamva ndipo anayamba kusangalala,+Midzi yozungulira Yuda inayamba kukondwera+Chifukwa cha zigamulo zanu, inu Yehova.+
9 Pakuti inu Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba wolamulira dziko lonse lapansi.+Mwakwera pamwamba kwambiri kuposa milungu ina yonse.+
10 Inu okonda Yehova+ danani nacho choipa.+Iye amateteza moyo wa anthu ake okhulupirika.+Amawalanditsa m’manja mwa anthu oipa.+
11 Kuwala kwaunikira wolungama,+Ndipo anthu owongoka mtima akusangalala.+
12 Sangalalani chifukwa cha Yehova, anthu olungama inu,+Ndipo yamikirani dzina lake loyera.*+
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “chikumbutso chake choyera.”