Mateyu 17:1-27

17  Patapita masiku 6 Yesu anatenga Petulo, Yakobo ndi Yohane m’bale wake, n’kukwera nawo m’phiri lalitali kwaokhaokha.+  Kumeneko iye anasandulika pamaso pawo, ndipo nkhope yake inawala ngati dzuwa.+ Malaya ake akunja anawala kwambiri.+  Kenako Mose ndi Eliya anaonekera kwa iwo akukambirana ndi Yesu.+  Ataona izi, Petulo anauza Yesu kuti: “Ambuye, ndi bwino ife tizikhala pano. Ngati mukufuna, ndimanga mahema atatu pano, limodzi lanu, limodzi la Mose ndi lina la Eliya.”+  Mawu ake adakali m’kamwa, mtambo wowala kwambiri unawaphimba, ndipo panamveka mawu kuchokera mumtambomo akuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndikukondwera naye,+ muzimumvera.”+  Ophunzirawo atamva zimenezi, anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi ndipo anachita mantha kwambiri.+  Kenako Yesu anawayandikira ndipo anawagwira n’kunena kuti: “Dzukani, musaope.”+  Atakweza maso awo, anaona kuti palibe wina aliyense koma Yesu yekha.+  Pamene anali kutsika m’phirimo, Yesu anawalamula kuti: “Musauze wina aliyense za masomphenya amenewa kufikira Mwana wa munthu ataukitsidwa kwa akufa.”+ 10  Koma ophunzirawo anamufunsa kuti: “Nanga n’chifukwa chiyani alembi amanena kuti Eliya ayenera kubwera choyamba?”+ 11  Poyankha iye anati: “Inde, Eliya adzabweradi ndipo adzabwezeretsa zinthu zonse.+ 12  Komabe, ine ndikukuuzani kuti Eliya anabwera kale ndipo iwo sanamuzindikire koma anam’chitira zilizonse zimene iwo anafuna. Momwemonso iwo adzazunza Mwana wa munthu.”+ 13  Pamenepo ophunzirawo anazindikira kuti anali kunena za Yohane M’batizi.+ 14  Tsopano atafika kufupi ndi khamu la anthu,+ mwamuna wina anamuyandikira, ndipo anam’gwadira ndi kunena kuti: 15  “Ambuye, muchitire chifundo mwana wanga wamwamuna, chifukwa ndi wakhunyu ndipo akuvutika kwambiri. Amagwera pamoto kawirikawiri ndiponso amagwera m’madzi kawirikawiri.+ 16  Ndinabwera naye kwa ophunzira anu, koma alephera kumuchiritsa.”+ 17  Poyankha Yesu anati: “Inu a m’badwo wopanda chikhulupiriro ndi wopotoka maganizo,+ kodi ndikhala nanube mpaka liti? Ndipitirize kukupirirani mpaka liti? Bwera nayeni kuno.” 18  Pamenepo Yesu anadzudzula chiwandacho, ndipo chinatuluka.+ Nthawi yomweyo mnyamatayo anachira.+ 19  Pambuyo pake ophunzira anabwera kwa Yesu paseri ndi kunena kuti: “N’chifukwa chiyani ife tinalephera kutulutsa chiwanda chija?”+ 20  Iye anawayankha kuti: “Chifukwa cha kuchepa kwa chikhulupiriro chanu. Pakuti ndithu ndikukuuzani, ngati mutakhala ndi chikhulupiriro chofanana ndi kanjere ka mpiru kuchepa kwake, mudzatha kuuza phiri ili kuti, ‘Choka pano upite apo,’ ndipo lidzachokadi. Palibe chimene chidzakhala chosatheka kwa inu.”+ 21 * —— 22  Atasonkhana pamodzi ku Galileya, Yesu anawauza kuti: “Mwana wa munthu adzaperekedwa m’manja mwa anthu,+ 23  ndipo adzamupha. Koma pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.”+ Atamva zimenezi iwo anamva chisoni kwambiri.+ 24  Atafika ku Kaperenao, anthu okhometsa msonkho wa madalakima awiri anafikira Petulo ndi kumufunsa kuti: “Kodi mphunzitsi wanu amapereka madalakima awiri a msonkho?”+ 25  Iye anati: “Inde amapereka.” Koma atalowa m’nyumba, asananene chilichonse, Yesu anamufunsa kuti: “Simoni, ukuganiza bwanji? Kodi mafumu a dziko lapansi amalandira ndalama za ziphaso kapena za msonkho kuchokera kwa ndani? Kuchokera kwa ana awo kapena kwa anthu achilendo?” 26  Atayankha kuti: “Kuchokera kwa anthu achilendo,” Yesu anamuuza kuti: “Choterotu ana sayenera kukhoma msonkho. 27  Koma kuti tisawakhumudwitse,+ pita kunyanja, ukaponye mbedza, ndipo ukatenge nsomba yoyambirira kuwedza. Ukakaikanula kukamwa kwake, ukapezako khobidi limodzi lasiliva.* Ukalitenge n’kukhomera msonkho wako ndi wanga.”+

Mawu a M'munsi

Mawu a vesi limeneli akupezeka m’Mabaibulo ena, koma mulibemo m’Baibulo lachigiriki la Westcott ndi Hort limene limagwirizana ndi mipukutu yakale kwambiri yachigiriki.
Mawu ake enieni “khobidi la siteta.” Khobidi limeneli linali lofanana ndi madalakima anayi.