Mateyu 23:1-39

23  Pambuyo pake Yesu analankhula kwa khamu la anthu ndi kwa ophunzira ake+ kuti:  “Alembi+ ndi Afarisi adzikhazika pampando wa Mose.+  Chotero muzichita ndi kutsatira zilizonse zimene angakuuzeni,+ koma musamachite zimene iwo amachita,+ chifukwa iwo amangonena koma osachita.  Iwo amamanga akatundu olemera ndi kusenzetsa anthu pamapewa,+ koma eni akewo safuna kusuntha akatunduwo ndi chala chawo.+  Zonse zimene amachita, amazichita kuti anthu awaone.+ Iwo amakulitsa timapukusi tokhala ndi malemba+ timene amavala monga zodzitetezera, ndipo amakulitsanso ulusi wopota wa m’mphepete+ mwa zovala zawo.  Amakonda malo olemekezeka kwambiri+ pa chakudya chamadzulo ndi mipando yakutsogolo m’masunagoge.+  Amakondanso kupatsidwa moni+ m’misika komanso kuti anthu aziwatchula kuti Rabi.+  Koma inu musamatchulidwe kuti Rabi, chifukwa mphunzitsi wanu ndi mmodzi yekha,+ ndipo nonsenu ndinu abale.  Komanso musamatchule aliyense kuti atate wanu padziko lapansi pano, pakuti Atate wanu ndi mmodzi,+ wakumwamba Yekhayo. 10  Musamatchedwe ‘atsogoleri,’+ pakuti Mtsogoleri wanu ndi mmodzi, Khristu. 11  Koma wamkulu kwambiri pakati panu akhale mtumiki wanu.+ 12  Aliyense wodzikweza adzatsitsidwa,+ koma aliyense wodzichepetsa adzakwezedwa.+ 13  “Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, onyenga inu! Chifukwa mukutseka+ ufumu wakumwamba kuti anthu asalowemo. Pakuti inuyo+ simukulowamo, mukuletsa amene akufuna kulowamo kuti asalowe. 14 * —— 15  “Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, onyenga inu!+ Chifukwa mumatha mitunda kuti mukatembenuze munthu mmodzi, koma akatembenuka mumam’sandutsa woyenera kuponyedwa m’Gehena* kuposa inuyo. 16  “Tsoka kwa inu atsogoleri akhungu,+ amene mumati, ‘Ngati munthu walumbirira kachisi palibe kanthu, koma ngati munthu walumbirira golide wa m’kachisi, asunge lumbiro lake.’+ 17  Opusa ndi akhungu inu! Chofunika kwambiri n’chiti, golide kapena kachisi amene wayeretsa golideyo?+ 18  Komanso mumati, ‘Ngati munthu walumbirira guwa lansembe, palibe kanthu, koma ngati munthu walumbirira mphatso imene ili paguwapo, asunge lumbiro lake.’ 19  Akhungu inu! Chofunika kwambiri n’chiti, mphatso kapena guwa lansembe+ limene limayeretsa mphatsoyo? 20  Chotero amene walumbirira guwa lansembe walumbirira guwalo ndi zonse zimene zili pamenepo, 21  ndipo amene walumbirira kachisi walumbirira kachisiyo limodzi ndi iye amene amakhala mmenemo.+ 22  Wolumbirira kumwamba walumbirira mpando wachifumu wa Mulungu+ komanso amene akukhala pampandowo. 23  “Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, onyenga inu! Chifukwa mumapereka chakhumi+ cha timbewu ta minti, dilili, ndi chitowe, koma mumanyalanyaza zinthu zofunika za m’Chilamulo, monga chilungamo,+ chifundo+ ndi kukhulupirika.+ Kupereka zinthu zimenezi n’kofunikadi, koma osanyalanyaza zinthu zinazo. 24  Atsogoleri akhungu inu,+ amene mumasefa zakumwa zanu kuti muchotsemo kanyerere+ koma mumameza ngamila.+ 25  “Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, onyenga inu! Chifukwa mumayeretsa kunja kwa kapu+ ndi mbale, koma mkati mwake mutadzaza zolanda+ ndi kusadziletsa. 26  Mfarisi wakhungu+ iwe, yeretsa mkati mwa kapu+ ndi mbale choyamba, kuti kunja kwakenso kukhale koyera. 27  “Tsoka inu alembi ndi Afarisi, onyenga inu!+ Chifukwa mumafanana ndi manda opaka laimu,+ amene kunja kwake amaonekadi okongola, koma mkati mwake muli mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zamitundu yonse. 28  Mofanana ndi zimenezi inunso, pamaso pa anthu, mumaonekadi ngati olungama+ koma mkati mwanu mwadzaza chinyengo ndi kusamvera malamulo. 29  “Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, onyenga inu!+ Chifukwa mumamanga manda a aneneri ndi kukongoletsa manda achikumbutso a anthu olungama,+ 30  ndipo mumanena kuti, ‘Tikanakhalako m’masiku a makolo athu, ifeyo sitikanakhudzidwa ndi mlandu wawo wokhetsa magazi a aneneri.’+ 31  Chotero mukudzichitira nokha umboni kuti ndinu ana a anthu amene anapha aneneri.+ 32  Choncho malizitsani ntchito+ imene makolo anu anayamba. 33  “Njoka inu, ana a mphiri,+ mudzathawa bwanji chiweruzo cha Gehena?+ 34  Pa chifukwa chimenechi, tsopano ndikukutumizirani+ aneneri, anthu anzeru ndi aphunzitsi.+ Ena a iwo mudzawapha+ ndi kuwapachika, ndipo ena mudzawakwapula+ m’masunagoge mwanu ndi kuwazunza mumzinda ndi mzinda, 35  kuti magazi onse olungama okhetsedwa padziko lapansi abwere pa inu,+ kuyambira magazi a Abele+ wolungama+ mpaka magazi a Zekariya mwana wa Barakiya, amene inu munamupha pakati pa nyumba yopatulika ndi guwa lansembe.+ 36  Ndithu ndikukuuzani kuti, Zinthu zonsezi zidzaubwerera m’badwo uwu.+ 37  “Yerusalemu, Yerusalemu, wakupha aneneri iwe+ ndi woponya miyala+ anthu otumizidwa kwa iwe.+ Mobwerezabwereza ndinafuna kusonkhanitsa ana ako pamodzi, muja nkhuku yathadzi imasonkhanitsira anapiye ake m’mapiko.+ Koma anthu inu simunafune zimenezo.+ 38  Tsopano tamverani! Mulungu wachoka n’kukusiyirani+ nyumba* yanuyi.+ 39  Ndithu ndikukuuzani, Kuyambira tsopano simudzandionanso kufikira pamene mudzanene kuti, ‘Wodalitsidwa iye wobwera m’dzina la Yehova!’”+

Mawu a M'munsi

Za mawu amene palibe, onani mawu a m’munsi pa Mt 17:21.
Onani Zakumapeto 6.
Kutanthauza kachisi.