Mika 3:1-12
3 Ine ndinapitiriza kunena kuti: “Tamverani inu atsogoleri a mbadwa za Yakobo ndi inu olamulira a nyumba ya Isiraeli.+ Kodi si inu oyenera kudziwa chilungamo?+
2 Inu mumadana ndi zinthu zabwino+ ndi kukonda zinthu zoipa.+ Mumasenda khungu la anthu ndi kuchotsa mnofu pamafupa awo.+
3 Mwadya mnofu wa anthu anga+ ndipo mwasenda khungu lawo. Mwaswa mafupa awo kukhala zidutswazidutswa. Mwawaphwanyaphwanya ngati mafupa ndi mnofu zimene zili mumphika wakukamwa kwakukulu komanso ngati nyama imene ili mumphika.+
4 Pa nthawiyo adzafuulira Yehova kuti awathandize, koma sadzawayankha.+ Adzawabisira nkhope yake pa nthawi imeneyo+ chifukwa cha zoipa zimene anali kuchita.+
5 “Yehova wanena zimene zidzachitikire aneneri amene akusocheretsa anthu a mtundu wanga.+ Aneneri amenewo akutafuna chakudya ndi mano awo+ n’kumanena kuti, ‘Mtendere!’+ Koma munthu akapanda kuika chakudya m’kamwa mwawo, amakonzekera kumuthira nkhondo.+ Kwa iwo Mulungu wanena kuti,
6 ‘Choncho anthu inu usiku udzakufikirani,+ ndipo simudzaonanso masomphenya.+ Mudzangoona mdima wokhawokha moti simudzaloseranso. Aneneri amenewa dzuwa lidzawalowera ndipo mdima udzawagwera masanasana.+
7 Oona masomphenya+ adzachita manyazi+ ndipo olosera+ adzakhumudwa ndithu. Onsewa adzaphimba ndevu zawo zapamlomo+ chifukwa Mulungu sadzawayankha.’”+
8 Koma ine ndili ndi mphamvu zochuluka chifukwa cha mzimu wa Yehova. Ndine wokonzeka kuchita zachilungamo ndi kusonyeza mphamvu+ kuti ndiuze mbadwa za Yakobo za kupanduka kwawo, komanso kuti ndiuze Isiraeli za tchimo lake.+
9 Tamverani izi inu atsogoleri a nyumba ya Yakobo komanso inu olamulira a nyumba ya Isiraeli,+ amene mukuipidwa ndi chilungamo ndiponso amene mukupotoza chilichonse chowongoka.+
10 Inu mukumanga Ziyoni ndi ntchito zokhetsa magazi ndipo mukumanga Yerusalemu mwa kuchita zinthu zopanda chilungamo.+
11 Atsogoleri a mumzindawo saweruza asanalandire chiphuphu+ ndipo ansembe ake amaphunzitsa kuti apeze malipiro.+ Aneneri ake amalosera kuti apeze ndalama.+ Komatu iwo amadalira Yehova ndipo amanena kuti: “Kodi Yehova sali pakati pathu?+ Choncho tsoka silidzatigwera.”+
12 Chotero Ziyoni adzagawulidwa ngati munda chifukwa cha anthu inu ndipo Yerusalemu adzangokhala milu ya mabwinja.+ Phiri la nyumba ya Mulungu lidzakhala ngati zitunda za m’nkhalango.