Miyambo 10:1-32
10 Miyambi ya Solomo.+
Mwana wanzeru amakondweretsa bambo ake,+ koma mwana wopusa amamvetsa chisoni mayi ake.+
2 Chuma cha anthu oipa chidzakhala chopanda phindu,+ koma chilungamo n’chimene chidzapulumutse munthu ku imfa.+
3 Yehova sadzachititsa munthu wolungama kukhala ndi njala,+ koma zolakalaka za anthu oipa adzazikankhira kumbali.+
4 Wogwira ntchito ndi dzanja laulesi adzakhala wosauka,+ koma dzanja la munthu wakhama ndi limene limalemeretsa.+
5 Mwana wozindikira amatuta m’chilimwe. Mwana wochititsa manyazi amakhala ali m’tulo tofa nato pa nthawi yokolola.+
6 Madalitso amapita pamutu pa wolungama,+ koma pakamwa pa anthu oipa pamabisa zachiwawa.+
7 Anthu akamakumbukira zabwino zimene munthu wolungama anali kuchita, amam’dalitsa,+ koma dzina la anthu oipa lidzawola.+
8 Munthu wanzeru mumtima mwake amamvera malamulo,+ koma wamilomo yopusa amaponderezedwa.+
9 Woyenda ndi mtima wosagawanika adzayenda popanda chomuopseza,+ koma wokhotetsa njira zake adzadziwika.+
10 Wotsinzinira ena ndi diso lake adzamvetsa ena ululu,+ ndipo wamilomo yopusa adzaponderezedwa.+
11 Pakamwa pa wolungama m’pamene pamachokera moyo,+ koma pakamwa pa anthu oipa pamabisa zachiwawa.+
12 Chidani n’chimene chimayambitsa mikangano,+ koma chikondi chimaphimba machimo onse.+
13 Pamilomo ya munthu womvetsa zinthu pamapezeka nzeru,+ koma ndodo amakwapulira msana wa munthu wopanda nzeru mumtima mwake.+
14 Anzeru ndiwo amapitiriza kuphunzira zinthu zamtengo wapatali,+ koma pakamwa pa wopusa patsala pang’ono kuwonongeka.+
15 Zinthu zamtengo wapatali za munthu wachuma zili ngati mudzi wake wolimba.+ Chiwonongeko cha onyozeka ndicho umphawi wawo.+
16 Zochita za wolungama zimabweretsa moyo.+ Zokolola za woipa zimabweretsa tchimo.+
17 Amene wagwira malangizo* mwamphamvu ndiye njira ya kumoyo,+ koma wosiya chidzudzulo amasocheretsa anthu.+
18 Pamene pali munthu wobisa chidani pamakhala milomo yonyenga,+ ndipo wobweretsa uthenga woipa ndi wopusa.+
19 Pakachuluka mawu sipalephera kukhala zolakwa,+ koma wodziwa kulamulira milomo yake amachita zinthu mwanzeru.+
20 Lilime la wolungama ndilo siliva wabwino kwambiri.+ Mtima wa woipa ndi wopanda phindu.+
21 Milomo ya wolungama imaweta anthu ambiri,+ koma zitsiru zimafa chifukwa chopanda nzeru mumtima.+
22 Madalitso a Yehova ndi amene amalemeretsa,+ ndipo sawonjezerapo ululu.+
23 Kwa wopusa, kusonyeza khalidwe lotayirira kuli ngati masewera,+ koma nzeru zimakhala ndi munthu wozindikira.+
24 Chinthu choopsa kwa woipa n’chimene chidzamubwerere,+ koma anthu olungama adzapatsidwa zimene amalakalaka.+
25 Woipa amatha ngati momwe zimakhalira pakawomba mphepo yamkuntho,+ koma wolungama ndiye maziko mpaka kalekale.*+
26 Monga mmene amakhalira vinyo wowawasa m’mano ndiponso utsi m’maso, ndi mmenenso amakhalira munthu waulesi kwa amene am’tuma.+
27 Kuopa Yehova kudzawonjezera masiku,+ koma zaka za anthu oipa zidzafupikitsidwa.+
28 Zoyembekezera za olungama zimasangalatsa,+ koma chiyembekezo cha oipa chidzawonongeka.+
29 Njira ya Yehova ndiyo malo achitetezo kwa munthu wopanda cholakwa,+ koma anthu ochita zopweteka ena adzawonongedwa.+
30 Wolungama sadzagwedezedwa mpaka kalekale,+ koma anthu oipa sadzapitiriza kukhala padziko lapansi.+
31 Pakamwa pa wolungama pamabala zipatso za nzeru,+ koma lilime lonena zopotoka lidzadulidwa.+
32 Milomo ya wolungama imavomerezedwa ndi Mulungu,*+ koma pakamwa pa anthu oipa m’popotoka.+