Miyambo 12:1-28

12  Wokonda malangizo* amakondanso kudziwa zinthu,+ koma wodana ndi chidzudzulo ndi wopanda nzeru.+  Munthu wabwino Yehova amakondwera naye,+ koma munthu wamaganizo oipa iye amamutcha woipa.+  Palibe munthu amene angakhazikike chifukwa chochita zoipa,+ koma muzu wa anthu olungama sudzagwedezedwa.+  Mkazi wabwino ndi chisoti cha ulemu kwa mwamuna wake,*+ koma mkazi wochita zinthu zochititsa manyazi ali ngati chowoletsa mafupa a mwamunayo.+  Maganizo a anthu olungama ndiwo chilungamo.+ Utsogoleri wa anthu oipa ndi wachinyengo.+  Mawu a anthu oipa amadikirira kukhetsa magazi,+ koma pakamwa pa anthu owongoka mtima m’pamene padzawapulumutse.+  Anthu oipa amagonjetsedwa n’kusakhalaponso,+ koma nyumba ya anthu olungama idzakhalapobe.+  Munthu adzatamandidwa chifukwa cha pakamwa pake panzeru,+ koma wa mtima wopotoka adzanyozedwa.+  Kuli bwino kukhala munthu wamba koma n’kukhala ndi wantchito, kusiyana n’kukhala wodzikuza koma wopanda chakudya.+ 10  Wolungama amasamalira moyo wa chiweto chake,+ koma chisamaliro cha anthu oipa n’chankhanza.+ 11  Wolima nthaka yake adzakhala ndi chakudya chokwanira,+ koma wofunafuna zinthu zopanda pake ndi wopanda nzeru mumtima mwake.+ 12  Woipa amalakalaka nyama yokodwa mumsampha wa anthu oipa,+ koma muzu wa anthu olungama umabala zipatso.+ 13  Munthu woipa amakodwa ndi kuchimwa kwa milomo yake,+ koma wolungama amachoka m’masautso.+ 14  Munthu amakhutitsidwa ndi zabwino kuchokera ku zipatso za pakamwa pake,+ ndipo zochita za manja a munthu, zidzabwerera kwa iye.+ 15  Njira ya munthu wopusa imakhala yolondola m’maso mwake,+ koma womvera malangizo ndi wanzeru.+ 16  Munthu amene amasonyeza mkwiyo wake tsiku lomwelo ndi wopusa,+ koma wochenjera akachitiridwa chipongwe, amangozinyalanyaza.+ 17  Wotulutsa mawu okhulupirika amanena zolungama,+ koma mboni yonama imanena zachinyengo.+ 18  Pali munthu amene amalankhula mosaganizira ndi mawu olasa ngati lupanga,+ koma lilime la anthu anzeru limachiritsa.+ 19  Mlomo wa choonadi+ ndi umene udzakhazikike kwamuyaya,+ koma lilime lachinyengo lidzangokhalapo kwa kanthawi.+ 20  Chinyengo chimakhala mumtima mwa anthu okonza chiwembu,+ koma olimbikitsa mtendere amasangalala.+ 21  Palibe chopweteka chimene chidzagwere wolungama,+ koma anthu oipa ndi amene tsoka lizidzangowagwera.+ 22  Milomo yonama imam’nyansa Yehova,+ koma anthu ochita zinthu mokhulupirika amam’sangalatsa.+ 23  Munthu wochenjera amabisa zimene akudziwa,+ koma mtima wa anthu opusa umalengeza zopusa.+ 24  Dzanja la anthu akhama n’limene lidzalamulire,+ koma dzanja laulesi lidzagwira ntchito yaukapolo.+ 25  Nkhawa mumtima mwa munthu ndi imene imauweramitsa,+ koma mawu abwino ndi amene amausangalatsa.+ 26  Wolungama amayendera msipu wake, koma njira ya anthu oipa imawachititsa kuyenda uku ndi uku.+ 27  Ulesi sungavumbulutse nyama zimene munthu akufuna kusaka,+ koma munthu wakhama ndiye chuma chamtengo wapatali cha munthu. 28  M’njira yachilungamo muli moyo,+ ndipo ulendo wa m’njira imeneyi suthera ku imfa.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.
Mawu ake enieni, “mwiniwake.”