Miyambo 14:1-35
14 Mkazi amene alidi wanzeru amamanga nyumba yake,+ koma wopusa amaigwetsa ndi manja ake.+
2 Munthu woyenda mowongoka mtima amaopa Yehova,+ koma munthu amene amayenda m’njira zokhotakhota amanyoza Mulungu.+
3 Chikwapu cha kudzikuza chili m’kamwa mwa wopusa,+ koma anthu anzeru milomo yawo imawatsogolera.+
4 Ngati palibe ng’ombe, chodyeramo chimakhala choyera. Koma zokolola zimachuluka chifukwa cha mphamvu za ng’ombe yamphongo.
5 Mboni yokhulupirika ndi imene sinama,+ koma mboni yonyenga imanena bodza lokhalokha.+
6 Munthu wonyoza amafunafuna nzeru ndipo sazipeza. Koma kudziwa zinthu kumakhala kosavuta kwa munthu womvetsa zinthu.+
7 Choka pamaso pa munthu wopusa,+ chifukwa supeza nzeru m’mawu otuluka pakamwa pake.+
8 Nzeru za munthu wochenjera ndizo kuzindikira njira imene akuyendamo,+ koma kuganiza mopusa kwa zitsiru ndi chinyengo.+
9 Anthu opusa akapalamula mlandu amangoseka,+ koma pakati pa anthu owongoka mtima pali mgwirizano.+
10 Mtima umadziwa kuwawa kwa moyo wa munthu,+ ndipo mlendo sangalowerere pamene mtimawo ukusangalala.
11 Nyumba za anthu oipa zidzawonongedwa,+ koma mahema a anthu owongoka mtima adzalemera.+
12 Pali njira yooneka ngati yowongoka kwa munthu,+ koma mapeto ake ndi imfa.+
13 Ngakhale pamene munthu akuseka, mtima wake ukhoza kukhala ukupweteka.+ Ndipo kusangalala kumathera m’chisoni.+
14 Munthu wa mtima wosakhulupirika adzakhutira ndi zotsatira za njira zake,+ koma munthu wabwino adzakhutira ndi zotsatira za zochita zake.+
15 Munthu amene sadziwa zinthu amakhulupirira mawu alionse,+ koma wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.+
16 Munthu wanzeru amachita mantha ndipo amapatuka pa choipa,+ koma wopusa amapsa mtima ndiponso amakhala wodzidalira.+
17 Munthu amene amakwiya msanga amachita zinthu zopusa,+ koma munthu wotha kuganiza bwino amadedwa.+
18 Anthu osadziwa zinthu, ndithu adzakhala opusa,+ koma kwa ochenjera, kudziwa zinthu kudzakhala ngati chovala cha kumutu.+
19 Anthu oipa adzagwadira abwino,+ ndipo oipa adzagwada pazipata za munthu wolungama.
20 Munthu wosauka amadedwa ngakhale ndi mnzake,+ koma munthu wolemera amakhala ndi anzake ambiri.+
21 Munthu wonyoza mnzake ndiye kuti akuchimwa,+ koma wodala ndi munthu wokomera mtima anthu osautsika.+
22 Anthu okonza chiwembu amasochera,+ koma anthu okonzekera kuchita zabwino amapeza kukoma mtima kosatha ndi choonadi.+
23 Kugwira ntchito iliyonse kumapindulitsa,+ koma kungolankhula mawu chabe kumasaukitsa.
24 Chisoti chaulemu cha anthu anzeru ndi chuma chawo. Zochita za anthu opusa zimawonjezera kupusa kwawo.+
25 Mboni yoona imapulumutsa anthu,+ koma mboni yonama imangonena bodza.+
26 Munthu woopa Yehova amakhulupirira Mulungu pa chilichonse,+ ndipo ana a munthu ameneyu adzapeza malo othawirako.+
27 Kuopa Yehova ndiko chitsime cha moyo,+ chifukwa kumateteza moyo kumisampha ya imfa.+
28 Kuchuluka kwa anthu kumakongoletsa mfumu,+ koma kuchepa kwa anthu kumawonongetsa nduna.+
29 Wosafulumira kukwiya n’ngozindikira zinthu kwambiri,+ koma wokwiya msanga amalimbikitsa uchitsiru.+
30 Mtima wodekha ndiwo moyo wa munthu,+ koma nsanje imawoletsa mafupa.+
31 Wobera munthu wosauka mwachinyengo amanyoza amene anamupanga,+ koma wokomera mtima munthu wosauka amalemekeza amene anamupanga.+
32 Woipa adzakankhidwa chifukwa cha kuipa kwake,+ koma wolungama adzapeza malo othawirako chifukwa cha mtima wake wosagawanika.+
33 Mumtima mwa munthu womvetsa zinthu mumakhala nzeru,+ ndipo zimadziwika pakati pa anthu opusa.
34 Chilungamo chimakweza mtundu wa anthu,+ koma tchimo limachititsa manyazi mitundu ya anthu.+
35 Mfumu imasangalala ndi wantchito wochita zinthu mozindikira,+ koma imakwiya ndi wantchito wochita zinthu zochititsa manyazi.+