Miyambo 15:1-33
15 Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo,+ koma mawu opweteka amayambitsa mkwiyo.+
2 Lilime la anthu anzeru limalankhula zabwino zimene anthuwo akudziwa,+ koma pakamwa pa zitsiru pamasefukira mawu opusa.+
3 Maso a Yehova ali paliponse.+ Amayang’ana anthu oipa ndi abwino omwe.+
4 Lilime lodekha lili ngati mtengo wa moyo,+ koma lilime lachinyengo limapweteketsa mtima.+
5 Aliyense wopusa amanyoza malangizo* a bambo ake,+ koma munthu aliyense womvera chidzudzulo ndi wochenjera.+
6 M’nyumba ya munthu wolungama muli katundu wambiri,+ koma katundu wa munthu woipa amabweretsa tsoka.+
7 Milomo ya anzeru imafalitsa zimene ikudziwa,+ koma mtima wa anthu opusa suchita zimenezo.+
8 Nsembe ya anthu oipa imam’nyansa Yehova,+ koma pemphero la anthu owongoka mtima limam’sangalatsa.+
9 Yehova amanyansidwa ndi njira ya munthu woipa,+ koma iye amakonda munthu wochita chilungamo.+
10 Munthu wosiya njira yabwino amadana ndi malangizo.+ Aliyense wodana ndi chidzudzulo adzafa.+
11 Manda ndiponso malo a chiwonongeko+ zili pamaso pa Yehova.+ Ndiye kuli bwanji mitima ya ana a anthu?+
12 Munthu wonyoza amadana ndi munthu amene akum’dzudzula.+ Iye sadzapita kwa anthu anzeru.+
13 Mtima wachimwemwe umapangitsa nkhope kusangalala,+ koma chifukwa cha kupweteka kwa mtima munthu sasangalala.+
14 Mtima womvetsa ndi umene umafunafuna kudziwa zinthu,+ koma pakamwa pa anthu opusa m’pamene pamafunafuna kulankhula zopusa.+
15 Masiku onse a munthu wosautsika amakhala oipa,+ koma munthu wamtima wosangalala amachita phwando nthawi zonse.+
16 Ndi bwino kukhala ndi zinthu zochepa ukuopa Yehova,+ kusiyana ndi kukhala ndi zinthu zambiri koma uli ndi nkhawa.+
17 Ndi bwino kudya zamasamba koma pali chikondi,+ kusiyana ndi kudya nyama ya ng’ombe yamphongo yodyetsedwa bwino pali chidani.+
18 Munthu wopsa mtima amayambitsa mkangano,+ koma munthu wosakwiya msanga amaziziritsa mkangano.+
19 Njira ya munthu waulesi ili ngati mpanda wa mitengo yaminga,+ koma njira ya anthu owongoka mtima imakhala yosalazidwa bwino.+
20 Mwana wanzeru ndi amene amakondweretsa bambo ake,+ koma wopusa amanyoza mayi ake.+
21 Munthu wopanda nzeru mumtima mwake amakondwera ndi uchitsiru,+ koma munthu wozindikira ndi amene amayenda panjira yabwino.+
22 Zolingalira sizikwaniritsidwa ngati anthu sakambirana moona mtima,+ koma aphungu akachuluka zimakwaniritsidwa.+
23 Munthu amasangalala ndi yankho lochokera pakamwa pake,+ ndipo mawu onenedwa pa nthawi yoyenera ndi abwino kwambiri.+
24 Njira ya kumoyo ndi yowongoka kwa munthu wochita zanzeru,+ kuti asatsikire pansi ku Manda.+
25 Yehova adzagwetsa nyumba za anthu odzikuza,+ koma adzakhazikitsa malire a malo a mkazi wamasiye.+
26 Ziwembu za munthu woipa ndi zonyansa kwa Yehova,+ koma mawu osangalatsa ndi oyera pamaso pake.+
27 Munthu wopeza phindu mwachinyengo amabweretsa tsoka panyumba pake,+ koma wodana ndi ziphuphu ndi amene adzakhalebe ndi moyo.+
28 Mtima wa munthu wolungama umayamba waganiza usanayankhe,+ koma pakamwa pa anthu oipa pamasefukira zoipa.+
29 Yehova amakhala kutali ndi anthu oipa,+ koma amamva pemphero la anthu olungama.+
30 Maso+ owala amapangitsa mtima kusangalala.+ Uthenga+ wabwino umanenepetsa mafupa.+
31 Munthu amene khutu lake limamvetsera chidzudzulo+ chopatsa moyo, amakhala pakati pa anthu anzeru.+
32 Aliyense wokana malangizo+ amakana moyo wake, koma munthu womvetsera chidzudzulo amakhala ndi mtima wanzeru.+
33 Kuopa Yehova ndi kumene kumaphunzitsa munthu kuchita zinthu mwanzeru,+ ndipo ulemerero umabwera pambuyo pa kudzichepetsa.+