Miyambo 18:1-24

18  Wodzipatula amafunafuna zolakalaka zake zosonyeza kudzikonda.+ Iye amachita zosemphana ndi nzeru zonse zopindulitsa.+  Aliyense wopusa sakondwera ndi kuzindikira zinthu,+ mpaka zimene zili mumtima mwake zitaululika.+  Mnyozo umabwera limodzi ndi munthu woipa,+ ndipo chitonzo chimabwera limodzi ndi manyazi.+  Mawu a m’kamwa mwa munthu ndiwo madzi akuya.+ Chitsime cha nzeru chili ngati mtsinje wosefukira.+  Kukondera munthu woipa si bwino.+ Komanso si bwino kukankhira pambali munthu wolungama poweruza.+  Milomo ya munthu wopusa imalowa mu mkangano,+ ndipo pakamwa pake pamaitana zikwapu.+  Pakamwa pa munthu wopusa m’pamene pamamuwononga,+ ndipo milomo yake ndi msampha wa moyo wake.+  Mawu a munthu wonenera ena zoipa ali ngati zinthu zofunika kuzimeza msangamsanga,+ zimene zimatsikira mkatikati mwa mimba.+  Komanso waulesi pa ntchito yake+ ndiye m’bale wake wa munthu wobweretsa chiwonongeko.+ 10  Dzina la Yehova ndi nsanja yolimba.+ Wolungama amathawira mmenemo ndipo amatetezedwa.+ 11  Zinthu zamtengo wapatali za munthu wachuma ndizo mzinda wake wolimba,+ ndipo m’maganizo mwake zili ngati mpanda woteteza.+ 12  Munthu asanagwe, mtima wake umadzikweza,+ ndipo asanapeze ulemerero, amadzichepetsa.+ 13  Munthu aliyense woyankhira nkhani asanaimvetsetse n’ngopusa,+ ndipo amachita manyazi.+ 14  Mtima wa munthu ukhoza kupirira matenda,+ koma mtima wosweka ndani angaupirire?+ 15  Mtima wa munthu womvetsa zinthu umadziwa zinthu,+ ndipo khutu la anzeru limafunafuna kudziwa zinthu.+ 16  Mphatso ya munthu imam’tsegulira khomo lalikulu,+ ndipo imakam’fikitsa ngakhale pamaso pa anthu olemekezeka.+ 17  Woyamba kufotokoza mbali yake pa mlandu amaoneka ngati wolondola,+ koma mnzake amabwera n’kumufufuzafufuza.+ 18  Maere amathetsa mikangano,+ ndipo amalekanitsa ngakhale anthu amphamvu.+ 19  M’bale amene walakwiridwa amaposa mzinda wolimba,+ ndipo pali mikangano imene imakhala ngati mtengo wotsekera pachipata cha nsanja yokhalamo.+ 20  Mimba ya munthu imakhuta zipatso za pakamwa pake.+ Iye amakhuta ngakhale zokolola za milomo yake.+ 21  Imfa ndiponso moyo zili mu mphamvu ya lilime,+ ndipo wolikonda adzadya zipatso zake.+ 22  Kodi munthu wapeza mkazi wabwino?+ Ndiye kuti wapeza chinthu chabwino,+ ndipo Yehova amakondwera naye.+ 23  Munthu wosauka amalankhula mochonderera,+ koma munthu wolemera amayankha mwamphamvu.+ 24  Pali mabwenzi amene amafuna kuthyolana,+ koma pali bwenzi limene limamatirira kuposa m’bale wako.+

Mawu a M'munsi