Miyambo 2:1-22
2 Mwana wanga, ukamvera mawu anga+ ndi kusunga malamulo anga ngati chuma chamtengo wapatali,+
2 ukamvetsera nzeru ndi khutu lako,+ ukaika mtima wako pa kuzindikira,+
3 komanso ukaitana kumvetsa zinthu+ ndi kufuulira kuzindikira,+
4 ukamazifunafuna ngati siliva,+ ndi kuzifufuza ngati chuma chobisika,+
5 udzamvetsa tanthauzo la kuopa+ Yehova ndipo udzamudziwadi Mulungu.+
6 Pakuti Yehova amapereka nzeru.+ Kudziwa zinthu ndi kuzindikira kumatuluka m’kamwa mwake.+
7 Anthu owongoka mtima, iye amawasungira nzeru zopindulitsa.+ Kwa anthu oyenda ndi mtima wosagawanika, iye amakhala chishango+
8 mwa kuyang’anitsitsa njira zachiweruzo,+ ndipo adzateteza njira ya anthu ake okhulupirika.+
9 Ukachita zimenezi udzamvetsa zinthu zolondola, zolungama, zowongoka, ndiponso njira yonse ya zinthu zabwino.+
10 Nzeru zikalowa mumtima mwako,+ ndipo kudziwa zinthu kukakhala kosangalatsa m’moyo wako,+
11 kuganiza bwino kudzakuyang’anira,+ ndipo kuzindikira kudzakuteteza,+
12 kuti kukupulumutse kunjira yoipa,+ ndiponso kwa munthu wonena zinthu zopotoka,+
13 komanso kwa anthu amene amasiya njira zowongoka kuti ayende m’njira za mdima.+
14 Kudzakupulumutsanso kwa anthu amene amasangalala kuchita zoipa,+ amene amakondwera ndi zinthu zoipa ndi zopotoka,+
15 amene njira zawo ndi zokhota ndiponso amene ali achinyengo m’zochita zawo zonse.+
16 Kudzakupulumutsa kwa mkazi wachilendo, mkazi wochokera kwina+ wolankhula mwaukathyali,+
17 amene wasiya mnzake wapamtima wa pachitsikana chake+ ndiponso amene waiwala pangano limene anapangana ndi Mulungu wake.+
18 Pakuti nyumba yake imatsikira kumanda ndipo njira zake zimatsikira kwa akufa.+
19 Onse ogona naye sadzabwerera ndipo iwo sadzapezanso njira za amoyo.+
20 Cholinga cha zonsezi n’chakuti uziyenda m’njira ya anthu abwino+ ndi kuti uzisunga njira za anthu olungama.+
21 Pakuti owongoka mtima ndi amene adzakhale m’dziko lapansi,+ ndipo opanda cholakwa ndi amene adzatsalemo.+
22 Koma oipa adzachotsedwa padziko lapansi+ ndipo achinyengo adzazulidwamo.+