Miyambo 20:1-30
20 Vinyo ndi wonyoza.+ Chakumwa choledzeretsa chimasokosera+ ndipo aliyense wosochera nacho alibe nzeru.+
2 Kuopsa kwa mfumu kuli ngati kubangula kwa mkango wamphamvu.+ Aliyense woputa mkwiyo wake akuchimwira moyo wake womwe.+
3 Kuleka kukangana kumabweretsa ulemerero kwa munthu,+ koma aliyense wopusa amafulumira kuyambitsa mkangano.+
4 Chifukwa cha kuzizira, waulesi salima.+ Iye azidzapemphapempha nthawi yokolola koma sadzapatsidwa kanthu.+
5 Maganizo a mumtima mwa munthu ali ngati madzi akuya,+ koma munthu wozindikira ndi amene amawatunga.+
6 Pakati pa anthu ambiri, aliyense amanena za kukoma mtima kwake kosatha,+ koma munthu wokhulupirika ndani angam’peze?+
7 Munthu wolungama amayenda ndi mtima wosagawanika,+ ndipo ana ake amakhala odala.+
8 Mfumu imakhala pampando wachiweruzo+ n’kubalalitsa zoipa zonse ndi maso ake.+
9 Ndani anganene kuti: “Ndayeretsa mtima wanga,+ ndadziyeretsa ku tchimo langa”?+
10 Miyezo iwiri yosiyana yoyezera kulemera kwa chinthu ndiponso miyezo iwiri yosiyana ya efa,*+ zonsezi n’zonyansa kwa Yehova.+
11 Ngakhale mnyamata amadziwika ndi ntchito zake, ngati zochita zake zili zoyera ndiponso zowongoka.+
12 Khutu lakumva ndiponso diso loona, zonsezi anazipanga ndi Yehova.+
13 Usamakonde tulo kuti ungasauke.+ Tsegula maso ako kuti ukhale ndi zakudya zambiri.+
14 Wogula amati, “Chinthu ichi n’choipa. N’choipa ichi!” Akatero amachoka.+ Kenako amakadzitama.+
15 Pali golide komanso miyala yamtengo wapatali ya korali yambirimbiri, koma milomo yodziwa zinthu ndiyo ziwiya zamtengo wapatali.+
16 Ngati munthu walonjeza kuti akhala chikole kwa mlendo,+ umulande chovala chake. Ndiponso wochita zoipa ndi mkazi wachilendo umulande chikole.+
17 Munthu amasangalala ndi chakudya chimene wachipeza mwachinyengo,+ koma pambuyo pake, m’kamwa mwake mumadzaza miyala.+
18 Zolinga zimakhazikika anthu akakambirana,+ ndipo uzitsatira malangizo anzeru pomenya nkhondo yako.+
19 Woyenda uku ndi uku n’kumanena zoipa za anthu ena amaulula zinsinsi,+ ndipo usamagwirizane ndi munthu wotengeka ndi milomo yake.+
20 Aliyense wotemberera bambo ake ndi mayi ake,+ nyale yake idzazimitsidwa kukagwa mdima.+
21 Cholowa chopezedwa mwadyera poyamba,+ tsogolo lake silidzadalitsidwa.+
22 Usanene kuti: “Ndidzabwezera choipa.”+ Khulupirira Yehova+ ndipo iye adzakupulumutsa.+
23 Miyezo iwiri yosiyana yoyezera kulemera kwa chinthu ndi yonyansa kwa Yehova,+ ndipo sikelo yachinyengo si yabwino.+
24 Mayendedwe a mwamuna wamphamvu amachokera kwa Yehova,+ koma kodi munthu wochokera kufumbi angazindikire bwanji njira yake?+
25 Umakhala msampha munthu wochokera kufumbi akathamangira kufuula kuti, “N’zoyera!”+ koma pambuyo polonjeza+ n’kumafuna kuganiziranso bwino.+
26 Mfumu yanzeru imabalalitsa anthu oipa,+ ndipo imawaponda ndi wilo lopunthira.+
27 Mpweya+ wa munthu wochokera kufumbi ndiwo nyale ya Yehova. Imafufuza mosamala mkatikati monse mwa mimba.+
28 Kukoma mtima kosatha ndiponso choonadi zimateteza mfumu,+ ndipo chifukwa cha kukoma mtima kosatha kumeneko mfumu imakhazikitsa mpando wake wachifumu.+
29 Kukongola kwa anyamata ndiko mphamvu zawo,+ ndipo ulemerero wa anthu okalamba ndiwo imvi zawo.+
30 Zilonda zobwera chifukwa chomenyedwa zimachotsa zoipa,+ ndipo zikwapu zimafika mpaka mkatikati mwa mimba.+
Mawu a M'munsi
^ Muyezo umodzi wa efa ndi wofanana ndi chitini cha malita 22.