Miyambo 22:1-29
22 Ndi bwino kusankha dzina labwino kusiyana ndi chuma chochuluka.+ Kulemekezedwa kuli bwino kuposa siliva ndi golide.+
2 Munthu wolemera ndiponso munthu wosauka n’chimodzimodzi.+ Amene anapanga onsewa ndi Yehova.+
3 Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala,+ koma anthu osadziwa zinthu amangopitabe ndipo amalangidwa.+
4 Zotsatirapo za kudzichepetsa ndiponso kuopa Yehova ndizo chuma, ulemerero, ndi moyo.+
5 Minga ndi misampha zimakhala m’njira ya munthu wochita zopotoka,+ koma woteteza moyo wake amakhala nazo kutali.+
6 Phunzitsa mwana m’njira yomuyenerera.+ Ngakhale akadzakalamba sadzapatukamo.+
7 Wolemera ndi amene amalamulira anthu osauka,+ ndipo wobwereka amakhala kapolo wa wobwereketsayo.+
8 Wofesa zosalungama adzakolola zopweteka,+ ndipo ndodo ya ukali wake idzatha.+
9 Wa diso labwino adzadalitsidwa, chifukwa amapereka chakudya chake kwa munthu wonyozeka.+
10 Thamangitsa wonyoza, kuti mikangano ithe ndiponso kuti milandu ndi kunyozedwa zilekeke.+
11 Amene amakondwera kukhala ndi mtima woyera+ ndiponso amene mawu ake ndi okopa, adzakhala bwenzi la mfumu.+
12 Maso a Yehova amateteza wodziwa zinthu,+ koma iye amawononga mawu a munthu wochita zachinyengo.+
13 Waulesi amati:+ “Panja pali mkango!+ Ndithu undipha pakati pa bwalo la mzinda!”
14 Pakamwa pa akazi achilendo pali ngati dzenje lakuya.+ Wotsutsidwa ndi Yehova adzagweramo.+
15 Uchitsiru umakhazikika mumtima mwa mwana.+ Koma ndodo yomulangira* ndi imene imauthamangitsira kutali ndi iye.+
16 Amene amabera mwachinyengo munthu wonyozeka kuti apeze zinthu zambiri,+ komanso wopereka mphatso kwa munthu wolemera, ndithu adzasauka.+
17 Tchera khutu lako ndi kumva mawu a anthu anzeru,+ kuti ulandire ndi mtima wonse nzeru zochokera kwa ine.+
18 Pakuti n’chinthu chosangalatsa kuti uzisunge mumtima mwako,+ kuti zikhazikike pamilomo yako.+
19 Lero ndakudziwitsa zinthu,+ kuti uzidalira Yehova.
20 Kodi sindinakulembere zinthu zolangiza ndi zophunzitsa,+
21 n’cholinga chakuti ndikusonyeze kudalirika kwa mawu oona, kuti uthe kubwezera mawu oonadi kwa amene wakutuma?+
22 Usabere munthu wonyozeka chifukwa chakuti ndi wonyozeka,+ ndipo usapondereze wosautsika pachipata cha mzinda.+
23 Pakuti Yehova adzawateteza pa mlandu wawo,+ ndipo adzalanda moyo wa amene akuwabera.+
24 Usamagwirizane ndi munthu aliyense wokonda kukwiya,+ ndipo usamayende ndi munthu waukali,
25 kuti usazolowere njira zake ndi kuikira moyo wako msampha.+
26 Usakhale pakati pa anthu ogwirana chanza,+ pakati pa anthu amene amakhala chikole cha ngongole za anthu ena.+
27 Ukadzalephera kulipira, adzakulanda ngakhale bedi limene umagonapo.
28 Usasunthire kumbuyo malire akalekale, amene makolo ako anaika.+
29 Kodi wamuona munthu waluso pa ntchito yake? Iye adzaima pamaso pa mafumu.+ Sadzaima pamaso pa anthu wamba.