Miyambo 25:1-28
25 Miyambi ina ya Solomo+ imene atumiki a Hezekiya mfumu ya Yuda+ anakopa, ndi iyi:
2 Ulemerero wa Mulungu ndiwo kusunga chinsinsi,+ ndipo ulemerero wa mafumu ndiwo kufufuza bwino nkhani.+
3 Kutalika kwa kumwamba,+ kuzama kwa dziko lapansi,+ ndiponso mtima wa mafumu, zonsezi n’zosatheka kuzifufuza.+
4 Siliva akachotsedwa zotsalira pomuyenga, yense adzatuluka woyengeka bwino.+
5 Woipa akachotsedwa pamaso pa mfumu,+ mpando wake wachifumu udzakhazikitsidwa ndi chilungamo.+
6 Usadzilemekeze wekha pamaso pa mfumu,+ ndipo usaime pamalo a anthu olemekezeka,+
7 pakuti ndi bwino kuti mfumuyo ikuuze kuti: “Bwera pamwamba pano,”+ kusiyana n’kuti ikutsitse pamaso pa munthu wolemekezeka amene wamuona ndi maso ako.+
8 Usamapite kukazenga mlandu mofulumira, pakuti udzachita chiyani pamapeto pake mnzakoyo akakuchititsa manyazi?+
9 Kambirana mlandu wako ndi mnzako,+ ndipo usaulule chinsinsi cha munthu wina,+
10 kuti amene akumvetsera angakuchititse manyazi ndiponso kuti nkhani yoipa imene iwe wanena ingavute kuiiwala.
11 Mawu olankhulidwa pa nthawi yoyenera ali ngati zipatso za maapozi agolide m’mbale zasiliva.+
12 Munthu wanzeru akamadzudzula munthu wa khutu lomvetsera, amakhala ngati ndolo* yagolide, ndiponso ngati chokongoletsera chagolide wapadera.+
13 Nthumwi yokhulupirika kwa anthu amene aituma ili ngati kuzizira kwa chipale chofewa+ pa tsiku lokolola, chifukwa imatsitsimula moyo wa ambuye ake.+
14 Munthu wodzitama kuti wapereka mphatso koma sanapereke, ali ngati mitambo ndi mphepo yopanda mvula.+
15 Kuleza mtima kumanyengerera mtsogoleri wa asilikali, ndipo lilime lofatsa likhoza kuthyola fupa.+
16 Ukapeza uchi udye wokukwanira,+ kuti usadye wambiri n’kuusanza.+
17 Phazi lako lisamapitepite kunyumba kwa mnzako, kuti angatope nawe n’kuyamba kudana nawe.
18 Munthu wonenera mnzake umboni wonama ali ngati chibonga cha kunkhondo, lupanga, ndi muvi wakuthwa.+
19 Kudalira munthu amene amachita zachinyengo pa tsiku la masautso kuli ngati dzino lothyoka ndi phazi lotsimphina.+
20 Wovula malaya pa tsiku lozizira ali ngati vinyo wowawasa wothiridwa mu soda, ndiponso ngati woimbira nyimbo munthu wa mtima wachisoni.+
21 Ngati munthu wodana nawe ali ndi njala, um’patse chakudya. Ngati ali ndi ludzu, um’patse madzi akumwa,+
22 pakuti ukumuunjikira makala amoto pamutu pake,+ ndipo Yehova adzakupatsa mphoto.+
23 Mphepo yochokera kumpoto imabweretsa mvula yambiri. Imakhala ngati kuti yabereka mvulayo ndi ululu wa pobereka.+ Chotero munthu wa lilime loulula chinsinsi amakhala ndi nkhope yonyozedwa.+
24 Kuli bwino kukhala pakona ya denga la nyumba, kusiyana ndi kukhala m’nyumba limodzi ndi mkazi wolongolola.+
25 Nkhani yabwino yochokera kudziko lakutali+ ili ngati madzi ozizira kwa munthu wotopa.+
26 Munthu wolungama akamanjenjemera pamaso pa munthu woipa, amakhala ngati kasupe woipitsidwa ndiponso chitsime chowonongedwa.+
27 Kudya uchi wambiri si bwino,+ ndipo anthu akamafunafuna okha ulemerero, kodi umenewo ndi ulemererodi?+
28 Munthu wosaugwira mtima ali ngati mzinda umene mpanda wake wagumulidwa, n’kuusiya wopanda mpanda.+
Mawu a M'munsi
^ Ena amati “masikiyo.”