Miyambo 3:1-35

3  Mwana wanga, usaiwale lamulo langa,+ ndipo mtima wako usunge malamulo anga.+  Ukatero, udzakhala ndi masiku ochuluka, moyo wazaka zambiri,+ ndi mtendere.+  Usasiye kukoma mtima kosatha ndi choonadi.+ Uzimange m’khosi mwako+ ndiponso uzilembe pamtima pako.+  Ukachita zimenezi, Mulungu ndi anthu adzakukomera mtima ndipo adzakuona kuti ndiwe wozindikira.+  Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse,+ ndipo usadalire luso lako lomvetsa zinthu.+  Uzim’kumbukira m’njira zako zonse,+ ndipo iye adzawongola njira zako.+  Usamadzione kuti ndiwe wanzeru.+ Uziopa Yehova ndi kupatuka pa choipa.+  Zimenezi zidzachiritsa+ mchombo wako ndi kutsitsimutsa mafupa ako.+  Uzilemekeza Yehova ndi zinthu zako zamtengo wapatali+ ndiponso ndi zipatso zako zonse zoyambirira.+ 10  Ukatero nkhokwe zako zidzakhala zodzaza+ ndipo zoponderamo mphesa zako zidzasefukira ndi vinyo watsopano.+ 11  Mwana wanga, usakane malangizo* a Yehova+ ndipo usanyansidwe ndi kudzudzula kwake,+ 12  chifukwa Yehova amadzudzula munthu amene amam’konda,+ monga momwe bambo amadzudzulira mwana amene amakondwera naye.+ 13  Wodala ndi munthu amene wapeza nzeru,+ ndiponso munthu amene wapeza kuzindikira,+ 14  chifukwa kupeza nzeru monga phindu n’kwabwino kuposa kupeza siliva monga phindu, ndipo kukhala nazo monga zokolola n’kwabwino kuposa kukhala ndi golide.+ 15  N’zamtengo wapatali kuposa miyala ya korali,+ ndipo zonse zimene umakonda sizingafanane nazo. 16  Masiku ochuluka ali m’dzanja lake lamanja.+ M’dzanja lake lamanzere muli chuma ndi ulemerero.+ 17  Njira zake n’zobweretsa chisangalalo ndipo misewu yake yonse ndi yamtendere.+ 18  Munthu akagwiritsitsa nzeru, zidzakhala ngati mtengo wa moyo+ kwa iye, ndipo ozigwiritsitsa+ adzatchedwa odala.+ 19  Yehova anayala maziko a dziko lapansi mwanzeru.+ Anakhazikitsa kumwamba mozindikira.+ 20  Chifukwa chakuti iye amadziwa zinthu, anagawa madzi akuya,+ ndipo kumwamba kwa mitambo kumagwetsa mvula yamawawa.+ 21  Mwana wanga, zimenezi zisachoke pamaso pako.+ Usunge nzeru zopindulitsa ndiponso kuganiza bwino,+ 22  ndipo zidzatanthauza moyo kwa iwe+ komanso zidzakhala chokongoletsa m’khosi mwako.+ 23  Ukatero udzayenda panjira yako popanda chokuopseza,+ ndipo ngakhale phazi lako silidzapunthwa ndi chilichonse.+ 24  Nthawi iliyonse ukagona sudzaopa chilichonse.+ Udzagona ndithu, ndipo tulo tako tidzakhala tokoma.+ 25  Sudzaopa zoopsa zilizonse zadzidzidzi,+ kapena mphepo yamkuntho yowomba oipa, chifukwa ikubwera.+ 26  Pakuti Yehova ndiye amene uzidzamudalira,+ ndipo adzateteza phazi lako kuti lisakodwe.+ 27  Usalephere kuchitira zabwino anthu amene akufunikira zabwinozo,+ pamene dzanja lako lingathe kuchita zimenezo.+ 28  Usanene kwa mnzako kuti, “Pita, ukabwerenso mawa ndidzakupatsa,” pamene uli ndi chinachake choti ungam’patse.+ 29  Usakonze zochitira mnzako choipa,+ pamene iye akuona kuti akukhala nawe mwamtendere.+ 30  Usakangane ndi munthu popanda chifukwa,+ ngati sanakuchitire choipa.+ 31  Usasirire munthu wachiwawa,+ kapena kusankha njira zake.+ 32  Pakuti munthu wochita zachiphamaso+ Yehova amanyansidwa naye,+ koma amakonda anthu owongoka mtima.+ 33  Temberero la Yehova lili panyumba ya munthu woipa,+ koma malo okhala anthu olungama, iye amawadalitsa.+ 34  Onyoza,+ iye amawanyoza,+ koma ofatsa amawakomera mtima.+ 35  Anzeru adzapeza ulemu,+ koma opusa amatama zinthu zimene zidzawachititse manyazi.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.