Miyambo 31:1-31
31 Mawu a Mfumu Lemueli, uthenga wamphamvu+ umene mayi ake anamupatsa pomuphunzitsa:+
2 Kodi ndikufuna ndikuuze chiyani mwana wanga? Kodi ndikufuna ndikuuze mawu otani iwe mwana wochokera m’mimba mwanga?+ Kodi ndikufuna ndikuuze mawu otani iwe mwana wa malonjezo anga?+
3 Usamapereke mphamvu zako kwa akazi,+ ndipo usamapereke njira zako ku zinthu zimene zimachititsa mafumu kufafanizidwa.+
4 N’kosayenera kwa mafumu iwe Lemueli, n’kosayenera kuti mafumu azimwa vinyo,+ kapena kuti akuluakulu olemekezeka azinena kuti: “Kodi chakumwa choledzeretsa chili kuti?”
5 Chifukwa angamwe n’kuiwala malamulo ndi kupondereza ufulu wa ana ovutika.+
6 Anthu inu, perekani chakumwa choledzeretsa kwa munthu amene watsala pang’ono kuwonongedwa+ ndi vinyo kwa anthu amene mtima wawo ukuwawa.+
7 Munthu amwe n’kuiwala umphawi wake, ndipo asakumbukirenso mavuto ake.
8 Tsegula pakamwa pako kuti ulankhulire munthu amene sangathe kudzilankhulira yekha,+ kuti uthandize onse amene atsala pang’ono kufa.+
9 Tsegula pakamwa pako, weruza mwachilungamo ndipo thandiza munthu wosautsika ndi wosauka pa mlandu wake.+
א [ʼAʹleph]
10 Mkazi wabwino, ndani angam’peze?+ Mtengo wake umaposa wa miyala yamtengo wapatali.
ב [Behth]
11 Mtima wa mwamuna wake* umamudalira, ndipo mwamunayo sasowa kalikonse.+
ג [Giʹmel]
12 Masiku onse a moyo wake, mkaziyo amapatsa mwamuna wakeyo zabwino osati zoipa.+
ד [Daʹleth]
13 Amafunafuna ulusi ndi nsalu, ndipo manja ake amagwira ntchito iliyonse mosangalala.+
ה [Heʼ]
14 Iye ali ngati ngalawa za munthu wamalonda.+ Amabweretsa chakudya chake kuchokera kutali.
ו [Waw]
15 Amadzukanso kudakali usiku,+ n’kupereka chakudya kwa banja lake ndipo atsikana ake antchito amawapatsa gawo lawo.+
ז [Zaʹyin]
16 Amakaona munda n’kuugula.+ Amalima munda wa mpesa chifukwa cha ntchito ya manja ake.+
ח [Chehth]
17 Amakhala wokonzeka kugwira ntchito yolimba, ndipo amalimbitsa manja ake.+
ט [Tehth]
18 Amaona kuti malonda ake akuyenda bwino. Nyale yake siizima usiku.+
י [Yohdh]
19 Amatambasulira manja ake ndodo yokulungako ulusi, ndipo manja ake amagwira ndodo yopotera chingwe.+
כ [Kaph]
20 Amatambasulira dzanja lake munthu wosautsika, ndipo manja ake amawatambasulira munthu wosauka.+
ל [Laʹmedh]
21 Kukamazizira, iye sadera nkhawa za banja lake chifukwa a m’banja lake onse amavala zovala zotentha.*+
מ [Mem]
22 Iye amadzipangira zoyala pabedi.+ Zovala zake zimakhala za nsalu zabwino ndiponso za ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira.+
נ [Nun]
23 Mwamuna wake*+ amadziwika pazipata,+ akakhala pansi pamodzi ndi akulu a m’dzikolo.
ס [Saʹmekh]
24 Iye amapanga zovala zamkati+ n’kuzigulitsa, ndipo amapanga malamba n’kuwapereka kwa amalonda.
ע [ʽAʹyin]
25 Mphamvu ndi ulemerero ndiye zovala zake,+ ndipo sada nkhawa akamaganizira zam’tsogolo.+
פ [Peʼ]
26 Amatsegula pakamwa pake mwanzeru,+ ndipo lamulo la kukoma mtima kosatha lili palilime lake.+
צ [Tsa·dhehʹ]
27 Iye amayang’anira zochitika za pabanja pake, ndipo sadya chakudya cha ulesi.+
ק [Qohph]
28 Ana ake amaimirira n’kumuuza kuti ndi wodala.+ Mwamuna wake amaimirira n’kumutamanda kuti:+
ר [Rehsh]
29 “Pali ana aakazi ambiri+ amene asonyeza kuti ndi akazi abwino, koma iweyo waposa onsewo.”+
ש [Shin]
30 Chikoka chikhoza kukhala chachinyengo+ ndipo kukongola kukhoza kukhala kopanda phindu,+ koma mkazi woopa Yehova ndi amene amatamandidwa chifukwa cha zochita zake.+
ת [Taw]
31 M’patseni zipatso za manja ake,+ ndipo ntchito zake zimutamande ngakhale m’zipata.+
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “mwiniwake.”
^ Mawu ake enieni, “zovala ziwiri.”
^ Mawu ake enieni, “mwiniwake.”