Miyambo 7:1-27

7  Mwana wanga, sunga mawu anga+ ndipo usunge malamulo anga ngati chuma chamtengo wapatali.+  Sunga malamulo anga kuti upitirize kukhala ndi moyo+ ndipo usunge lamulo langa ngati mwana+ wako wa diso.  Uwamange kuzala zako,+ ndipo uwalembe pamtima pako.+  Uza nzeru+ kuti: “Ndiwe mlongo wanga,” ndipo kumvetsa zinthu ukutche “M’bale wanga wamkazi,”  kuti utetezedwe kwa mkazi wachilendo,+ ndiponso kwa mkazi wochokera kwina amene amalankhula mawu okopa.+  Pakuti ndinayang’ana pansi kuchokera pawindo* la nyumba yanga,+  kuti ndione anthu osadziwa zinthu.+ Ndinkafuna kuona mnyamata wopanda nzeru mumtima mwake amene anali pakati pa ana aamuna.+  Mnyamatayo anali kuyenda mumsewu pafupi ndi mphambano yopita kunyumba ya mkazi wachilendo. Iye anali kuyenda panjira yopita kunyumba ya mkaziyo,+  pa nthawi ya madzulo kuli kachisisira,+ kutatsala pang’ono kuda. 10  Ndinaona mkazi akubwera kudzakumana naye atavala zovala zosonyeza kuti ndi hule.+ Mkaziyo anali wamtima wachinyengo, 11  wolongolola ndiponso wamakani.*+ Mapazi ake sakhala m’nyumba mwake.+ 12  Amapezeka panja, m’mabwalo a mzinda,+ ndiponso amakhala akudikirira anthu pafupi ndi mphambano iliyonse.+ 13  Iye wagwira mnyamatayo n’kumupsompsona.+ Kenako, m’maso muli gwaa! akuyamba kumuuza kuti: 14  “Ndinayenera kupereka nsembe zachiyanjano.+ Lero ndakwaniritsa zimene ndinalonjeza.+ 15  N’chifukwa chake ndabwera kudzakumana nawe, kudzafunafuna nkhope yako kuti ndikupeze. 16  Ndayala zofunda pabedi panga. Ndayalaponso nsalu za ku Iguputo zamitundu yosiyanasiyana.+ 17  Ndawaza pabedi panga zonunkhiritsa za mule, aloye ndi sinamoni.+ 18  Bwera tisonyezane chikondi mpaka chitikwane. Tichite zimenezi mpaka m’mawa. Tisangalatsane pouzana mawu achikondi.+ 19  Pakuti mwamuna wanga sali kunyumba. Iye wayenda ulendo wopita kutali.+ 20  Wanyamula chikwama cha ndalama m’manja mwake. Iye adzabwera kunyumba tsiku limene mwezi udzakhale wathunthu.” 21  Mkaziyo wamusocheretsa mnyamatayo pochita zinthu zambiri zomukopa.+ Wamunyengerera ndi milomo yake yotulutsa mawu okopa.+ 22  Mwadzidzidzi mnyamatayo wayamba kulondola mkaziyo+ ngati ng’ombe yamphongo yopita kokaphedwa, ndiponso ngati kuti wamangidwa m’matangadza kuti alandire chilango* cha munthu wopusa. 23  Iye akulondola mkaziyo mpaka muvi utaboola chiwindi* chake,+ ngati mbalame yothamangira kumsampha,+ ndipo iye sakudziwa kuti zikukhudza moyo wake.+ 24  Tsopano ananu ndimvereni, ndipo mverani mawu otuluka m’kamwa mwanga.+ 25  Mtima wako usapatukire kunjira zake. Iweyo usayendeyende m’njira zake.+ 26  Pakuti mkaziyo waphetsa anthu ambiri,+ ndipo onse amene aphedwa ndi iye ndi ochuluka.+ 27  Nyumba yake ndiyo njira ya ku Manda.+ Imatsikira kuzipinda za imfa.+

Mawu a M'munsi

“Pawindo” limeneli panali potchingidwa ndi timatabwa tolukanalukana.
Ena amati “wanthota.”
Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.
Ena amati “mphafa.”