Miyambo 9:1-18
9 Nzeru yeniyeni+ yamanga nyumba yake.+ Yasema zipilala zake 7.
2 Yapha nyama yake ndipo yasakaniza vinyo wake. Kuwonjezera apo, yayala patebulo pake.+
3 Yatuma antchito ake aakazi kuti apite pamwamba pa zitunda za m’mudzi akaiitanire anthu, kuti:
4 “Aliyense wosadziwa zinthu apatukire kuno.”+ Aliyense wopanda nzeru mumtima mwake,+ nzeru* ikumuuza kuti:
5 “Bwerani mudzadye chakudya changa ndiponso mudzamwe nawo vinyo amene ndasakaniza.+
6 Alekeni anthu osadziwa zinthu kuti mupitirize kukhala ndi moyo,+ ndipo yendani mowongoka m’njira yomvetsa zinthu.”+
7 Amene amalangiza wonyoza amadzichotsera yekha ulemu,+ ndipo amene amadzudzula woipa amadzibweretsera chilema.+
8 Usadzudzule wonyoza kuti angadane nawe.+ Dzudzula munthu wanzeru ndipo adzakukonda.+
9 Pereka malangizo kwa munthu wanzeru ndipo adzawonjezera nzeru zake.+ Phunzitsa munthu wolungama ndipo adzapitiriza kuphunzira.
10 Kuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru.+ Kudziwa Woyera Koposa, ndiko kumvetsa zinthu.+
11 Pakuti ine ndidzachititsa kuti masiku ako akhale ambiri+ ndipo zaka za moyo wako zidzawonjezeredwa.+
12 Ngati wakhala wanzeru, nzeruzo zidzapindulitsa iweyo.+ Ngati uli wonyoza, iweyo ndiye udzavutike.+
13 Mkazi wopusa amakhala wolongolola.+ Iye ndi woperewera nzeru ndipo sadziwa chilichonse.+
14 Wakhala pampando pakhomo la nyumba yake, pachitunda cha m’mudzimo,+
15 kuti aziitana anthu odutsa amene akuyenda panjira zawo atalunjika kutsogolo. Iye akuwauza kuti:+
16 “Aliyense amene ali wosadziwa zinthu apatukire kuno.”+ Aliyense amene ali wopanda nzeru mumtima mwake,+ mkaziyo wamuuza kuti:
17 “Madzi akuba amatsekemera,*+ ndipo mkate wakudya mwakabisira umakoma.”+
18 Koma mwamunayo sakudziwa kuti kumeneko kuli akufa, ndiponso kuti amene amaitanidwa ndi mkaziyu ali kumalo otsika a ku Manda.+
Mawu a M'munsi
^ M’Chiheberi, nzeru akuitenga ngati munthu wamkazi m’chaputala chino.
^ Ena amati “amanzuna.”