Mlaliki 4:1-16
4 Ine ndinaganiziranso kuponderezana+ konse kumene kukuchitika padziko lapansi pano, ndipo ndinaona misozi ya anthu amene akuponderezedwa,+ koma panalibe wowatonthoza.+ M’manja mwa oponderezawo munali mphamvu, moti oponderezedwawo analibe wowatonthoza.
2 Ndinazindikira kuti anthu amene anafa kale ali bwino kuposa anthu amene ali moyo.+
3 Koma amene ali bwino kuposa onsewa ndi amene sanabadwe,+ amene sanaone ntchito yosautsa mtima imene ikuchitika padziko lapansi pano.+
4 Ineyo ndaona ntchito yonse imene anthu amaigwira mwakhama ndiponso imene amaigwira bwino,+ kuti imabweretsa mpikisano pakati pa anthu.*+ Izinso n’zachabechabe ndipo zili ngati kuthamangitsa mphepo.
5 Wopusa amapinda manja+ ake ndipo amadziwononga yekha.+
6 Kupuma pang’ono* kuli bwino kuposa kugwira ntchito mwakhama* ndi kuthamangitsa mphepo.+
7 Ine ndinaganiziranso zachabechabe zochitika padziko lapansi pano:
8 Pali munthu amene ali yekhayekha, wopanda mnzake.+ Alibenso mwana kapena m’bale wake,+ koma amangokhalira kugwira ntchito mwakhama. Komanso maso ake sakhutira ndi chuma.+ Iye amafunsa kuti: “Kodi ntchito yovutayi ndikugwirira ndani n’kumadzimana zinthu zabwino?”+ Izinso n’zachabechabe ndiponso ndi ntchito yosautsa mtima.+
9 Awiri amaposa mmodzi,+ chifukwa amapeza mphoto yabwino pa ntchito yawo imene amaigwira mwakhama.+
10 Ngati mmodzi wa iwo atagwa, winayo akhoza kum’dzutsa mnzakeyo.+ Koma kodi zingakhale bwanji munthu mmodzi atagwa popanda wina woti am’dzutse?+
11 Komanso, anthu awiri akagona pamodzi, amamva kutentha. Koma kodi mmodzi yekha angamve bwanji kutentha?+
12 Ngati wina angagonjetse munthu mmodzi, anthu awiri akhoza kulimbana naye.+ Ndipo chingwe chopotedwa ndi zingwe zitatu sichingaduke msanga.
13 Mwana wosauka koma wanzeru ali bwino+ kuposa mfumu yokalamba koma yopusa,+ imene sionanso kufunika kochenjezedwa.+
14 Pakuti mwanayo amatuluka m’ndende n’kukhala mfumu,+ ngakhale kuti anabadwa ngati wosauka mu ufumuwo.+
15 Ndaona anthu onse amoyo amene amayenda padziko lapansi pano. Ndaonanso mmene zimakhalira ndi mwana amene amalowa m’malo mwa mfumu.+
16 Ngakhale kuti anthu amene anali kumbali yake anali ambiri,+ pambuyo pake sadzakhutira naye,+ pakuti zimenezinso n’zachabechabe ndipo zili ngati kuthamangitsa mphepo.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “imachitika chifukwa cha mpikisano pakati pa anthu.”
^ Mawu ake enieni, “kupuma kodzaza dzanja limodzi.”
^ Mawu ake enieni, “ntchito yovuta yodzaza manja awiri.”