Nehemiya 1:1-11

1  Awa ndi mawu a Nehemiya+ mwana wa Hakaliya. M’mwezi wa Kisilevi,*+ m’chaka cha 20,+ ine ndinali kunyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani.+  Ndiyeno Haneni+ mmodzi mwa abale anga anabwera pamodzi ndi amuna ena kuchokera ku Yuda. Ndinawafunsa+ mmene zinthu zinalili kwa gulu la Ayuda+ amene anathawa+ ku ukapolo+ komanso ndinawafunsa za Yerusalemu.  Chotero anandiuza kuti: “Anthu otsala amene ali m’chigawo,*+ amene anathawa ku ukapolo, ali pamavuto aakulu+ ndipo akunyozedwa.+ Nawonso mpanda+ wa Yerusalemu unagwa ndipo zipata+ zake zinatenthedwa ndi moto.”  Ndiyeno nditangomva mawu amenewa, ndinakhala pansi n’kuyamba kulira. Kwa masiku angapo ndinali kulira, kusala kudya+ ndi kupemphera pamaso pa Mulungu wakumwamba.+  Pamenepo ndinati: “Inu Yehova Mulungu wakumwamba, ndinu Mulungu wamkulu ndi wochititsa mantha.+ Anthu amene amakukondani+ ndi kusunga malamulo anu+ mumawasungira pangano+ ndi kuwasonyeza kukoma mtima kosatha.  Chonde, tsegulani maso anu ndi kutchera khutu+ kuti mumve pemphero la ine mtumiki wanu+ limene ndikupemphera pamaso panu lero. Usana ndi usiku+ ndikupempherera atumiki anu, ana a Isiraeli. Pochita zimenezi ndikuvomereza+ machimo+ a ana a Isiraeli amene tinakuchimwirani. Tonse tinachimwa, ine pamodzi ndi nyumba ya bambo anga.+  Mosakayikira tachita zinthu zolakwika pamaso panu+ ndipo sitinasunge malamulo,+ malangizo+ ndi zigamulo+ zimene munapatsa mtumiki wanu Mose.+  “Chonde, kumbukirani+ mawu amene munauza mtumiki wanu Mose kuti, ‘Mukadzachita zinthu mosakhulupirika, ndidzakumwazani pakati pa anthu a mitundu ina.+  Mukadzabwerera kwa ine+ ndi kusunga malamulo anga,+ ngakhale anthu omwazikana a mtundu wanu atakhala kumalekezero a kumwamba, ndidzawasonkhanitsa kuchokera kumeneko+ ndi kuwabweretsa+ kumalo amene ndasankha kuikako dzina langa.’+ 10  Iwo ndi atumiki anu+ ndi anthu anu,+ amene munawawombola ndi mphamvu zanu zazikulu+ ndi dzanja lanu lamphamvu.+ 11  Aa, Yehova. Chonde, tcherani khutu ku pemphero la ine mtumiki wanu ndiponso pemphero+ la atumiki anu amene amasangalala ndi kuopa dzina lanu.+ Chonde, ndithandizeni ine mtumiki wanu kuti zinthu zindiyendere bwino lero+ ndipo mwamunayu andimvere chisoni.”+ Pa nthawi imeneyi, ine ndinali woperekera chikho+ kwa mfumu.

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 13.
N’kutheka kuti chimenechi chinali chigawo cha Yuda.