Nehemiya 10:1-39

10  Tsopano amene anatsimikizira panganoli ndi chidindo+ chawo ndi awa: Nehemiya+ amene ndiye Tirisata,+ mwana wa Hakaliya,+Komanso Zedekiya,  Seraya,+ Azariya, Yeremiya,  Pasuri, Amariya, Malikiya,  Hatusi, Sebaniya, Maluki,  Harimu,+ Meremoti, Obadiya,  Danieli,+ Ginetoni, Baruki,  Mesulamu, Abiya, Miyamini,  Maaziya, Biligai ndi Semaya. Amenewa anali ansembe.  Panalinso Alevi awa amene anatsimikizira panganoli: Yesuwa,+ mwana wamwamuna wa Azaniya, Binui wochokera pakati pa ana a Henadadi,+ Kadimiyeli, 10  ndi abale awo awa, Sebaniya,+ Hodiya, Kelita, Pelaya, Hanani, 11  Mika, Rehobu, Hasabiya, 12  Zakuri, Serebiya,+ Sebaniya, 13  Hodiya, Bani ndi Beninu. 14  Atsogoleri awa a anthu anatsimikiziranso panganoli: Parosi, Pahati-mowabu,+ Elamu, Zatu, Bani, 15  Buni, Azigadi, Bebai, 16  Adoniya,* Bigivai, Adini, 17  Ateri, Hezekiya, Azuri, 18  Hodiya, Hasumu, Bezai, 19  Harifi,* Anatoti, Nebai, 20  Magipiasi, Mesulamu, Heziri, 21  Mesezabele, Zadoki, Yaduwa, 22  Pelatiya, Hanani, Anaya, 23  Hoshiya, Hananiya, Hasubu, 24  Halohesi, Pila, Sobeki, 25  Rehumu, Hasabina, Maaseya, 26  Ahiya, Hanani, Anane, 27  Maluki, Harimu ndi Bana. 28  Ndiyeno anthu ena onse, ansembe,+ Alevi,+ alonda a pazipata,+ oimba,+ Anetini,+ ndi aliyense amene anadzipatula kwa mitundu ya anthu a m’mayikowo+ kuti asunge chilamulo+ cha Mulungu woona, akazi awo, ana awo aamuna ndi ana awo aakazi ndi aliyense wodziwa zinthu ndi wozindikira,+ 29  anali kumamatirabe kwa abale awo,+ anthu otchuka.+ Iwo anali kudzilowetsa m’lumbiro limene likanatha kuwabweretsera temberero.+ Lumbiro+ limenelo linali lakuti tidzatsatira chilamulo cha Mulungu woona+ chimene chinaperekedwa kudzera mwa Mose mtumiki wa Mulungu woona, ndi kusunga+ malamulo onse, zigamulo ndi mfundo+ za Yehova Ambuye wathu,+ 30  kutinso tisapereke ana athu aakazi kwa mitundu ya anthu ya m’dzikoli, ndiponso tisatenge ana awo aakazi ndi kuwapereka kwa ana athu aamuna.+ 31  Kunena za mitundu ya anthu a m’dzikolo+ imene inali kudzagulitsa katundu ndi mbewu zamtundu uliwonse* pa sabata, tinalumbira kuti sitigula kalikonse kuchokera kwa iwo pa sabata+ kapena pa tsiku lililonse lopatulika.+ Tinalumbiranso kuti sitiyenera kulima minda yathu m’chaka cha 7,+ ndipo tiyenera kukhululukira ngongole wina aliyense.+ 32  Kuwonjezera apo, tinadziikira malamulo akuti chaka chilichonse aliyense wa ife azipereka gawo limodzi mwa magawo atatu a sekeli kuti ndalama zimenezo akazigwiritsire ntchito pa utumiki wa panyumba ya Mulungu wathu.+ 33  Akazigwiritsire ntchito pokonza mkate wosanjikiza,+ nsembe yachikhalire yambewu,+ nsembe yachikhalire yopsereza ya pa tsiku la sabata+ ndi tsiku lokhala mwezi.+ Akazigwiritsirenso ntchito pokonza madyerero a pa nthawi yoikidwiratu,+ zinthu zopatulika+ ndi nsembe yamachimo+ yophimbira machimo a Isiraeli komanso pa ntchito zonse za panyumba ya Mulungu wathu.+ 34  Komanso tinachita maere+ okhudza ansembe, Alevi ndi anthu oti azibweretsa nkhuni+ kunyumba ya Mulungu wathu, mogwirizana ndi nyumba ya makolo athu, pa nthawi zoikidwiratu, chaka ndi chaka kuti aziziyatsira moto paguwa lansembe la Yehova Mulungu wathu,+ malinga ndi zimene zinalembedwa m’chilamulo.+ 35  Tinachita maerewo kuti tipezenso wobweretsa kunyumba ya Yehova zipatso zoyamba kucha m’dziko lathu+ chaka ndi chaka, ndi zipatso zoyamba kucha mwa zipatso zonse za mtengo uliwonse.+ 36  Kutinso azibweretsa ana aamuna oyamba kubadwa+ mwa ana athu ndi ziweto+ zathu malinga ndi zolembedwa m’chilamulo.+ Komanso kuti azibweretsa ana oyamba kubadwa a ng’ombe ndi nkhosa+ zathu kunyumba ya Mulungu wathu, kwa ansembe amene anali kutumikira m’nyumba ya Mulungu wathu.+ 37  Komanso tinafunika kupititsa ufa woyambirira wamisere,+ zopereka zathu,+ zipatso za mtengo uliwonse,+ vinyo watsopano+ ndi mafuta+ kwa ansembe kumalo odyera+ m’nyumba ya Mulungu wathu. Tinafunikanso kupititsa chakhumi kwa Alevi+ pa zinthu zochokera m’nthaka yathu, pakuti Aleviwo anali kulandira chakhumi kuchokera m’mizinda yathu yonse ya zaulimi. 38  Wansembe, mwana wamwamuna wa Aroni, azikhala ndi Alevi pamene iwo akulandira chakhumi.* Aleviwo azipereka gawo limodzi mwa magawo 10 a chakhumicho kunyumba ya Mulungu+ wathu kuzipinda zodyera+ m’nyumba yosungiramo zinthu. 39  Pakuti ana a Isiraeli ndi ana a Alevi ayenera kubweretsa zopereka+ zambewu, vinyo watsopano+ ndi mafuta kuzipinda zodyera. Kumeneku ndi kumene kuli ziwiya za kumalo opatulika ndi ansembe amene anali kutumikira,+ olondera pazipata+ ndi oimba,+ ndipo tisanyalanyaze nyumba ya Mulungu wathu.+

Mawu a M'munsi

Zikuoneka kuti ameneyu ndi Adonikamu wotchulidwa pa Eza 2:13.
Zikuoneka kuti ameneyu ndi Hasumu wotchulidwa pa Eza 2:19.
Zimenezi mwina zinali tirigu kapena barele.
Kapena kuti “gawo limodzi mwa magawo 10.”