Nehemiya 4:1-23

4  Tsopano Sanibalati+ atangomva kuti tinali kumanganso mpanda, anakhumudwa ndi kukwiya kwambiri,+ ndipo anali kunyoza+ Ayuda.  Iye anayamba kuuza abale ake+ ndi gulu lankhondo la ku Samariya kuti: “Kodi Ayuda ofookawa akuchita chiyani? Kodi akuona ngati akwanitsa chintchito chomanga chimenechi? Kodi adzapereka nsembe?+ Kodi amaliza kumangako tsiku limodzi? Kodi adzachita kufukula miyala imene inatenthedwa ndi kuigwiritsiranso ntchito?”+  Tsopano Tobia+ Muamoni,+ anali pamodzi ndi Sanibalati ndipo anati: “Ngakhaletu nkhandwe+ itakwera pampanda wamiyala umene akumangawo ingathe kuugwetsa ndithu.”  Ndiyeno Nehemiya anati: “Inu Mulungu wathu, imvani+ mawu onyoza amene akutinenera.+ Bwezerani chitonzo chawocho+ pamutu pawo ndipo apititseni m’dziko laukapolo monga zofunkha.  Musanyalanyaze cholakwa chawo+ ndi machimo amene anakuchitirani. Musawafafanizire machimowo chifukwa akhumudwitsa anthu omanga mpandawo.”  Choncho tinapitiriza kumanga mpandawo, ndipo khoma lonse linalumikizana mpaka kufika hafu ya kutalika kwake. Anthu anapitiriza kukhala ndi mtima wogwira ntchito.+  Ndiyeno Sanibalati,+ Tobia,+ Aluya,+ Aamoni+ ndi Aasidodi+ atamva kuti ntchito yokonza mpanda wa Yerusalemu ikupita patsogolo, pakuti malo ogumuka anali atayamba kutsekedwa, anakwiya kwambiri.  Choncho onsewa anayamba kukonza chiwembu+ kuti abwere kudzamenyana ndi Yerusalemu ndi kudzatisokoneza.  Koma tinapemphera+ kwa Mulungu wathu, ndipo chifukwa cha adani amenewa, tinaika alonda kuti azititeteza usana ndi usiku. 10  Ndiyeno anthu a ku Yuda anayamba kunena kuti: “Mphamvu za anthu onyamula katundu+ zatha, koma pali zinyalala zambiri zofunika kuchotsa,+ ndipo ife sitingathe kumanga mpandawu tokha.” 11  Komanso adani athu anali kunena kuti: “Sadzadziwa+ kapena kuona kuti tikubwera, kufikira titafika pakati pawo ndipo tidzawapha ndithu ndi kuimitsa ntchito yomangayo.” 12  Ndiyeno pamene Ayuda okhala pafupi ndi adani amenewo anabwera anatiuza maulendo okwana 10 kuti: “Adaniwo adzabwera kumene ife tikukhala, kumenenso inu mudzabwera, ndipo adzatiukira kuchokera kumbali zonse.” 13  Choncho ndinaika amuna kuseli kwa mpanda pamalo otsika ndiponso oonekera. Ndinaikanso anthu onyamula malupanga,+ mikondo ing’onoing’ono+ ndi mauta malinga ndi mabanja awo. 14  Nditaona kuti akuchita mantha, nthawi yomweyo ndinanyamuka ndi kuuza anthu olemekezeka,+ atsogoleri+ ndi anthu onse kuti: “Musachite nawo mantha+ anthu amenewa. Kumbukirani Yehova, Mulungu wamkulu+ ndi wochititsa mantha.+ Menyerani nkhondo abale anu,+ ana anu aamuna, ana anu aakazi, akazi anu ndi nyumba zanu.” 15  Tsopano adani athuwo anamva kuti tadziwa za chiwembu chawo, mwakuti Mulungu woona anasokoneza cholinga chawo.+ Zitatero tonse tinabwerera ku ntchito yomanga mpanda, aliyense pa ntchito yake. 16  Kuchokera pamene adaniwo anamva kuti chiwembu chawo chadziwika mpaka m’tsogolo, hafu ya anyamata anga+ inali kalikiliki pa ntchito ndipo hafu yotsalayo inali kunyamula mikondo ing’onoing’ono, zishango, mauta ndipo inali kuvala zovala za mamba achitsulo.+ Ndipo akalonga+ anali kuima kumbuyo kwa Ayuda ndi kumawachirikiza. 17  Koma omanga mpandawo ndi anthu amene anali kunyamula katundu wolemera, aliyense wa iwo anali kalikiliki kugwira ntchito ndi dzanja limodzi ndipo kudzanja lina+ anali kunyamula mkondo.+ 18  Aliyense wa omangawo anali atamangirira lupanga lake m’chiuno+ pamene anali kumanga+ mpandawo, ndipo munthu woliza lipenga la nyanga ya nkhosa+ anali pambali panga. 19  Ndiyeno ndinauza anthu olemekezeka, atsogoleri+ ndi anthu ena onse kuti: “Ntchito yakula kwambiri ndipo tamwazikana kuzungulira mpandawu. 20  Mukamva kwina kukulira lipenga la nyanga ya nkhosa, musonkhane kumeneko, ndipo ife tidzakhala tili kumeneko. Mulungu wathu adzatimenyera nkhondo.”+ 21  Pamene hafu ya amunawo inali kalikiliki kugwira ntchito, hafu ina inali kunyamula mikondo ing’onoing’ono kuyambira m’bandakucha mpaka usiku nyenyezi zitatuluka. 22  Kuwonjezera apo, pa nthawiyo ndinauza anthu kuti: “Mwamuna aliyense pamodzi ndi mtumiki wake azigona mu Yerusalemu,+ ndipo usiku azikhala alonda athu koma masana azigwira ntchito.” 23  Koma ine,+ abale anga,+ atumiki anga+ ndi amuna olondera+ amene anali pambuyo panga, sitinali kuvula zovala zathu, ndipo aliyense anali ndi mkondo+ m’dzanja lake lamanja.

Mawu a M'munsi