Numeri 11:1-35

11  Tsopano anthuwo anayamba kudandaula pamaso pa Yehova ngati kuti anali pamavuto.+ Yehova atamva kudandaulako anawapsera mtima, ndipo moto wa Yehova unawayakira n’kupsereza ena a iwo kumalire a msasa.+  Koma pamene anthuwo anayamba kulirira Mose, iye anapembedzera Yehova+ ndipo motowo unazima.  Malo amenewo anawatcha Tabera,*+ chifukwa moto wa Yehova unawayakira pamalo amenewo.  Tsopano khamu la anthu a mitundu yosiyanasiyana+ lomwe linali pakati pawo linasonyeza mtima wadyera,+ ndipo ana a Isiraeli nawonso anayamba kulira n’kumanena kuti: “Ndani atipatse nyama yoti tidye?+  Tikukumbukira nsomba zaulere zimene tinali kudya ku Iguputo,+ nkhaka, mavwende, adyo komanso anyezi wamitundumitundu!  Koma tsopano tilibe ndi mphamvu zomwe. Maso athu sakuonanso kanthu kena, koma mana basi.”+  Manawo+ anali ngati mapira,*+ ndipo maonekedwe ake anali ngati utomoni woonekera mkati ngati galasi.+  Anthuwo anali kumwazikana kukatola manawo.+ Akatero, ankawapera pamphero kapena kuwasinja mumtondo. Kenako ankawawiritsa mumphika,+ kapena kuwapanga makeke ozungulira. Kukoma kwake anali ngati keke yotsekemera* yothira mafuta.+  Mame akagwa pamsasa usiku, mananso ankagwa.+ 10  Tsopano Mose anamva anthu akulira m’mabanja mwawo, munthu aliyense pakhomo la hema wake. Pamenepo mkwiyo wa Yehova unawayakira koopsa anthuwo.+ Mose nayenso anaipidwa nazo zimenezo.+ 11  Ndiyeno Mose anadandaulira Yehova kuti: “N’chifukwa chiyani mwandivutitsa chonchi ine mtumiki wanu? N’chifukwa chiyani mwandiumira mtima chotere, n’kundisenzetsa chimtolo cha anthu onsewa?+ 12  Kodi ndine ndinatenga pakati pa anthu onsewa? Ndine kodi ndinawabereka, kuti mundiuze kuti, ‘Uwafukate pachifuwa chako+ mmene mlezi amafukatira mwana woyamwa,’+ pa ulendo wopita nawo kudziko limene munalumbirira makolo awo?+ 13  Ndiitenga kuti nyama yoti ndipatse anthu onsewa? Pakuti iwo akupitirizabe kundilirira ine, kuti, ‘Tipatse nyama yoti tidye!’ 14  Sindingathe kuwasamalira ndekha anthuwa, chifukwa iwo ndi chimtolo chimene sindingathe kuchisenza.+ 15  Ngati umu ndi mmene muchitire ndi ine, ndikomereni mtima chonde, ingondiphani kuti tsokali lindichoke.”+ 16  Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Undisonkhanitsire akulu 70 mwa akulu a Isiraeli,+ amene ukuwadziwa kuti ndiwo akulu ndi oyang’anira pakati pa anthuwo.+ Upite nawo kuchihema chokumanako, ndipo akaime kumeneko limodzi nawe. 17  Ine nditsikira kumeneko+ kudzalankhula nawe.+ Ndidzatengako gawo lina la mzimu+ umene uli pa iwe n’kuuika pa iwo. Pamenepo iwo adzatha kukuthandiza kusenza udindo woyang’anira anthuwo, kuti usausenze wekhawekha.+ 18  Ndipo uuze anthuwo kuti, ‘Mudziyeretse pokonzekera tsiku lamawa,+ pakuti mudya nyama. Paja mwakhala mukulirira Yehova,+ kuti: “Ndani atipatse nyama yoti tidye? Ku Iguputo zinthu zinali kutiyendera bwino.”+ Nyamayo Yehova akupatsani ndithu, ndipo muidyadi.+ 19  Imeneyo simuidya tsiku limodzi, kapena masiku awiri, kapena masiku asanu, kapena masiku 10, kapenanso masiku 20 ayi, 20  koma mudzaidya kwa mwezi wonse wathunthu, mpaka idzatulukira m’mphuno mwanu, ndipo mudzachita kunyansidwa nayo.+ Zidzatero chifukwa mwakana Yehova amene ali pakati panu, ndipo mukum’lirira kuti: “Tinachokeranji ku Iguputo?”’”+ 21  Koma Mose anati: “Amuna amene ndikuyenda nawo akukwana 600,000,+ koma inuyo mukunena kuti, ‘Nyamayo ndiwapatsa, ndipo adzaidya kwa mwezi wonse wathunthu.’ 22  Kodi tiwaphera ziweto zonse kuti ziwakwanire?+ Kapena tiwaphera nsomba zonse za m’nyanja kuti ziwakwanire?” 23  Ndiyeno Yehova anamuyankha Mose kuti: “Kodi dzanja la Yehova lafupika lero eti?+ Tsopano uona ngati zimene ndanena zichitikedi kapena ayi.”+ 24  Pamenepo Mose anapita kukauza anthuwo mawu a Yehova. Anasonkhanitsa amuna 70 kuchokera pa akulu a anthuwo, n’kuwauza kuti aimirire mozungulira chihema chokumanako.+ 25  Kenako Yehova anatsika mumtambo+ n’kulankhula naye.+ Anatengako gawo lina la mzimu+ umene unali pa Mose n’kuuika pa aliyense wa akulu 70 amenewo. Ndipo mzimuwo utangokhala pa iwo, anayamba kuchita zinthu ngati aneneri, koma sanadzachitenso kachiwiri.+ 26  Tsopano panali amuna awiri amene anatsalira mumsasa. Wina dzina lake anali Eledadi, ndipo winayo anali Medadi. Mzimuwo unatsika pa amenewanso, chifukwa anali pakati pa olembedwawo, ngakhale kuti sanapite nawo kuchihema chokumanako kuja. Choncho iwonso anayamba kuchita zinthu ngati aneneri mumsasamo. 27  Pamenepo mnyamata wina anathamanga kukanena kwa Mose, kuti: “Eledadi ndi Medadi akuchita zinthu ngati aneneri mumsasa.” 28  Pamenepo, Yoswa mwana wa Nuni, yemwe anali mtumiki+ wa Mose kuyambira ali mnyamata, anayankhira kuti: “Mbuyanga Mose, kawaletseni amenewo!”+ 29  Koma Mose anayankha kuti: “Kodi ukuchita nsanje chifukwa chondidera nkhawa? Ayi usatero. Ndikanakonda anthu onse a Yehova akanakhala aneneri, chifukwa Yehova akanaika mzimu wake pa iwo!”+ 30  Pambuyo pake, Mose limodzi ndi akulu a Isiraeliwo anabwerera kumsasa. 31  Kenako Yehova anautsa mphepo+ yamkokomo kuchokera kunyanja. Mphepoyo inabweretsa zinziri,+ ndipo inazimwaza kuyambira pamsasapo mpaka pamtunda woyenda tsiku limodzi kulowera mbali ina, ndiponso mtunda woyenda tsiku limodzi kulowera mbali inayo. Inazimwaza kuzungulira msasawo, moti zinali kuuluka m’munsi kwambiri pafupifupi mikono* iwiri kuchokera pansi. 32  Ndiyeno anthuwo anayamba kugwira zinzirizo. Anazigwira masana onse mpaka usiku wonse, mpakanso tsiku lotsatira osalekeza. Amene anagwira zokwana mahomeri* 10+ ndiwo amene anagwira zochepa. Ndipo anali kuziyanika paliponse, moti zinangoti mbwee, pamsasa wonsewo. 33  Nyamayo ikadali m’kamwa mwawo,+ asanaitafune, mkwiyo wa Yehova unawayakira+ anthuwo. Ndipo Yehova anayamba kuwakantha anthuwo n’kuwapha ambiri.+ 34  Malo amenewo anawatcha Kibiroti-hatava,+ chifukwa anafotserapo anthu amene anasonyeza mtima wadyera.+ 35  Anthuwo atachoka pa Kibiroti-hatava, anasamukira ku Hazeroti,+ ndipo anakhala kumeneko.

Mawu a M'munsi

Dzina limeneli limatanthauza “Kuyaka; Moto Walawilawi.”
Mawu ake enieni, “njere ya koriyanda.” Koriyanda ndi chomera chimene ena amati “masala,” ndipo njere yake ndi yoyera ngati mapira.
Ena amati “kunzuna.”
“Mkono umodzi” ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu.
“Homeri” imodzi ndi yofanana ndi malita 220.