Numeri 12:1-16

12  Tsopano Miriamu ndi Aroni anayamba kum’nena Mose chifukwa cha mkazi wachikusi amene anam’kwatira.+  Iwo ankanena kuti: “Kodi Yehova walankhula kudzera kwa Mose yekha? Kodi sanalankhulenso kudzera kwa ife?”+ Koma Yehova anali kumvetsera.+  Moseyo anali munthu wofatsa kwambiri+ kuposa anthu onse amene anali padziko lapansi.  Kenako Yehova anauza Mose, Aroni ndi Miriamu kuti: “Nonse atatu nyamukani, mupite kuchihema chokumanako.” Pamenepo atatuwo ananyamuka n’kupita.  Tsopano Yehova anatsika mumtambo woima njo ngati chipilala+ n’kuima pakhomo la chihema chokumanako, ndipo anaitana Aroni ndi Miriamu. Pamenepo iwo anayandikira kumeneko.  Iye anawauza kuti: “Mvetserani mawu anga. Pakanakhala mneneri wa Yehova pakati panu, ndikanamudziwitsa za ine m’masomphenya,+ ndipo ndikanalankhula naye m’maloto.+  Koma sindikutero ndi mtumiki wanga Mose.+ Iye ndamuikiza nyumba yanga yonse.+  Ndimalankhula naye pamasom’pamaso,+ kumuuza zinthu momveka bwino osati mophiphiritsa,+ ndipo amaona maonekedwe a Yehova.+ Tsopano n’chifukwa chiyani inu simunaope kum’nena Mose mtumiki wanga?”+  Pamenepo Yehova anawakwiyira koopsa, n’kuchokapo. 10  Kenako mtambo uja unachoka pamwamba pa chihemacho. Pomwepo, Miriamu anagwidwa ndi khate loyera mbuu!+ Aroni atacheuka, anangoona kuti Miriamu wachita khate.+ 11  Atangoona choncho, Aroni anachonderera Mose kuti: “Pepani mbuyanga, chonde, musawerengere tchimo limene tachita mopusali.+ 12  Chonde, musangomulekerera Miriamu kuti akhale ngati mwana wobadwa wakufa,+ wotuluka m’mimba mwa amayi ake mnofu wake utawola mbali ina.” 13  Pamenepo Mose anayamba kufuulira Yehova kuti: “Chonde Mulungu wanga! M’chiritseni chonde!”+ 14  Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Kodi bambo ake akanam’lavulira+ malovu kumaso, sakanakhala wonyazitsidwa masiku 7? Choncho m’tulutseni+ akakhale kunja kwa msasa masiku 7,+ pambuyo pake mum’landire mumsasamo.”+ 15  Chotero Miriamu anatulutsidwa kukakhala kunja kwa msasa masiku 7,+ ndipo anthuwo sanasamuke kufikira Miriamu atalandiridwanso mumsasa. 16  Pambuyo pake, anthuwo anachoka ku Hazeroti,+ n’kukamanga msasa m’chipululu cha Parana.+

Mawu a M'munsi