Numeri 22:1-41
22 Kenako, ana a Isiraeli anasamuka kumaloko n’kukamanga msasa m’chipululu cha Mowabu,+ moyang’anana ndi Yeriko patsidya pa mtsinje wa Yorodano.
2 Tsopano Balaki+ mwana wa Zipori, anaona zonse zimene Aisiraeli anachita kwa Aamori.
3 Amowabu anachita mantha kwambiri ndi anthuwo chifukwa cha kuchuluka kwawo. Iwo anagwidwa mantha aakulu poopa ana a Isiraeliwo.+
4 Pamenepo Amowabu anakalankhula ndi akuluakulu a ku Midiyani,+ kuti: “Chikhamuchi chidzamwetula malo athu onse monga ng’ombe yomwetula msipu kubusa.”
Pa nthawi imeneyo, Balaki+ mwana wa Zipori ndiye anali mfumu ya Mowabu.
5 Tsopano iye anatumiza amithenga kwa Balamu,+ mwana wa Beori, ku Petori+ pafupi ndi Mtsinje*+ wa m’dziko lawo. Anawatuma kuti akamuitane, kuti: “Taonani! Anthu ochokera ku Iguputo afika kuno. Iwo adzaza dziko lino kulikonse kumene munthu angayang’ane,+ ndipo akukhala pafupi penipeni moyang’anana ndi ine.
6 Tsopano tabwerani chonde, mudzanditembererere+ anthuwa chifukwa ndi amphamvu kuposa ineyo, kuti mwina ndingawagonjetse n’kuwapitikitsa m’dziko lino. Ndikudziwa kuti munthu amene inu mwamudalitsa, amakhaladi wodalitsika, ndipo munthu amene mwamutemberera, amakhaladi wotembereredwa.”+
7 Chotero, akuluakulu a ku Mowabu ndi a ku Midiyani anapita kwa Balamu+ atatenga malipiro okamulipira kuti awawombezere maula,+ komanso anamuuza zimene Balaki ananena.
8 Balamu atamva mawuwo anawawuza kuti: “Gonani konkuno lero. Ndikuyankhani malinga n’zimene Yehova ati andiuze.”+ Akalonga a ku Mowabuwo anagonadi kwa Balamu.
9 Kenako Mulungu anafika kwa Balamu n’kumufunsa kuti:+ “Kodi anthu uli nawowa ndani?”
10 Balamu anayankha Mulungu woonayo kuti: “Balaki+ mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu, ndi amene watumiza anthuwa kuti adzandiitane kuti,
11 ‘Taonani! Anthu amene achokera ku Iguputo adzaza dziko lino kulikonse kumene munthu angayang’ane.+ Tsopano bwerani, mudzanditembererere anthuwa,+ kuti mwina ndingathe kumenyana nawo n’kuwathamangitsa.’”
12 Koma Mulungu anauza Balamu kuti: “Usapite nawo, ndipo anthuwo usakawatemberere,+ pakuti iwo ndi odalitsidwa.”+
13 M’mawa mwake Balamu atadzuka, anauza akalonga a Balakiwo kuti: “Pitani kudziko lakwanu, chifukwa Yehova wakana zoti ndipite nanu.”
14 Pamenepo akalonga a ku Mowabu aja ananyamuka n’kubwerera kwa Balaki, ndipo anakamuuza kuti: “Balamu wakana kubwera nafe.”+
15 Koma Balaki anatumizanso akalonga ena, ochulukirapo komanso olemekezeka kuposa oyamba aja.
16 Awanso anapita kwa Balamu n’kumuuza kuti: “Balaki mwana wa Zipori akuti: ‘Chonde, pasakhale chokuletsani kubwera kwa ine.
17 Ndithu ndidzakupatsani ulemerero waukulu,+ ndipo chilichonse chimene mungandiuze ndidzachita.+ Chonde tabwerani mudzanditembererere anthuwa.’”
18 Koma Balamu anayankha atumiki a Balaki aja kuti: “Ngakhale Balaki atandipatsa nyumba yake yodzaza siliva ndi golide, sindingachite chilichonse mosemphana ndi zimene Yehova Mulungu wanga angandilamule, kaya kuchotsera kapena kuwonjezerapo.+
19 Bwanji inunso mugone konkuno usiku wa lero, kuti ndimve zimene Yehova andiuze ulendo uno.”+
20 Usikuwo Mulungu anafika kwa Balamu, n’kumuuza kuti: “Ngati anthuwa abwera kudzakuitana, nyamuka, pita nawo limodzi. Koma ukalankhule mawu okhawo amene ndikakuuze.”+
21 M’mawa kutacha, Balamu anadzuka n’kumanga chishalo pabulu* wake, ndipo anapita limodzi ndi akalonga a ku Mowabu aja.+
22 Tsopano Mulungu anapsa mtima poona kuti Balamu akupita, moti mngelo wa Yehova anaima pamsewu kuti amutchingire njira.+ Balamuyo anali pabulu wake, ndipo anali ndi anyamata ake awiri.
23 Ndiyeno buluyo anaona mngelo wa Yehova ali chilili pamsewu lupanga lake lili m’manja.+ Pamenepo buluyo anayesetsa kupatukira kumbali kwa msewu kuti adutse kutchire, koma Balamu anayamba kum’kwapula kuti am’bwezere mumsewu.
24 Mngelo wa Yehovayo anakaimanso panjira yopanikiza yodutsa pakati pa minda ya mpesa. Njirayo inali ndi khoma la miyala uku ndi uku.
25 Buluyo anaonanso mngelo wa Yehova uja. Ndipo anayamba kudzikanikizira kukhoma, moti anakanikiziranso phazi la Balamu kukhomako. Pamenepo, Balamu anayamba kum’kwapulanso kwambiri bulu uja.
26 Tsopano mngelo wa Yehova anasunthiranso patsogolo. Anakaima pamalo ena opanikiza, pomwe panalibiretu mpata woti n’kudutsira kudzanja lamanja kapena lamanzere.
27 Buluyo ataonanso mngelo wa Yehova, tsopano anangokhala pansi, Balamu ali pamsana pake. Pamenepo Balamu anapsa mtima koopsa,+ ndipo anayamba kum’kwapulanso ndi ndodo yake.
28 Potsirizira pake, Yehova anatsegula pakamwa pa buluyo,+ ndipo buluyo anafunsa Balamu kuti: “Kodi ndakulakwirani chiyani kuti mundikwapule katatu konseka?”+
29 Balamu anayankha buluyo kuti: “Chifukwa wandichita nkhanza kwambiri. Moti ndikanakhala ndi lupanga m’dzanja langa, bwenzi pano n’takupha!”+
30 Buluyo anafunsanso Balamu kuti: “Kodi si ine bulu wanu amene mwakhala mukukwera moyo wanu wonse mpaka lero? Kodi ndinayamba ndachitapo zimenezi kwa inu?”+ Iye anayankha kuti: “Iyayi!”
31 Tsopano Yehova anatsegula maso a Balamu,+ ndipo iye anaona mngelo wa Yehova ali chilili panjirapo, lupanga lili m’manja. Nthawi yomweyo, Balamu anagwada pansi n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi.
32 Ndiyeno mngelo wa Yehova uja anam’funsa kuti: “N’chifukwa chiyani wakhala ukukwapula bulu wako maulendo atatu onsewa? Inetu ndabwera kudzakutchingira njira, chifukwa uli pa ulendo wothamangira kukachita zotsutsana ndi chifuniro changa.+
33 Koma buluyu wandiona, ndipo wayesa kundipewa maulendo atatu onsewa.+ Akanapanda kundipewa, ndithu, bwenzi pano n’takupha.+ Koma buluyu n’kanamusiya kuti akhale ndi moyo.”
34 Balamu atamva zimenezi anauza mngelo wa Yehovayo kuti: “Ndachimwa,+ sindinadziwe kuti inuyo munaima pamsewu kudzakumana nane. Bwanji ndibwerere ngati sizinakusangalatseni?”
35 Koma mngelo wa Yehovayo anauza Balamu kuti: “Pita nawo limodzi anthuwa,+ koma ukanene zokhazo zimene ndikuuze.”+ Choncho Balamu anapitiriza ulendo wake limodzi ndi akalonga a Balakiwo.
36 Balaki atamva kuti Balamu wafika, nthawi yomweyo ananyamuka kukamulandira kumzinda wa Mowabu. Mzindawu unali pafupi ndi mtsinje wa Arinoni, umene unali kumalire a dzikolo.+
37 Ndiyeno Balaki anafunsa Balamu kuti: “Kodi sindinatumize amithenga kuti adzakuitaneni? Nanga n’chifukwa chiyani simunabwere? Kodi mukuganiza kuti ineyo sindingathe kukupatsani ulemerero wochuluka?”+
38 Balamu anayankha Balaki kuti: “Si ine ndabwerane! Inetu sindingathe kunena kalikonse.+ Mawu amene Yehova ati aike m’kamwa mwangamu ndi amene ndilankhule.”+
39 Chotero Balamu anatengana ndi Balaki, n’kupita ku Kiriyati-huzoti.
40 Kumeneko Balaki anapereka nsembe za nyama ya ng’ombe ndi nkhosa,+ n’kutumiza ina kwa Balamu ndi akalonga amene anali nawo limodzi.
41 M’mawa kutacha, Balaki anakatenga Balamu n’kupita naye ku Bamoti-baala.+ Anam’tengera kumeneko kuti akathe kuliona bwino khamu lonse la Aisiraeli.+