Numeri 25:1-18

25  Tsopano Aisiraeli anali kukhala ku Sitimu.+ Ali kumeneko, iwo anayamba kuchita chiwerewere ndi akazi a ku Mowabu.+  Akaziwo ankabwera kudzaitana Aisiraeliwo kuti azipita nawo limodzi kokapereka nsembe kwa milungu yawo.+ Kumeneko, Aisiraeliwo ankadya ndi kugwadira milungu ya Amowabuwo.+  Chotero Aisiraeli anayamba kupembedza nawo Baala wa ku Peori.+ Pamenepo, mkwiyo wa Yehova unawayakira.+  Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Gwira onse amene akutsogolera anthuwo, uwaphe ndipo mitembo yawo uindandalike padzuwa pamaso pa Yehova.+ Uchite zimenezo kuti mkwiyo wa Yehova umene wayakira Aisiraeli uchoke.”  Chotero Mose anauza oweruza a mu Isiraeli+ kuti: “Aliyense wa inu aphe+ anthu ake amene akukapembedza nawo Baala wa ku Peori.”  Kenako anthuwo anangoona mwamuna wina wachiisiraeli+ akubwera ndi mkazi wachimidiyani.+ Anali kubwera naye kufupi ndi abale ake, pamaso pa Mose ndi pamaso pa khamu lonse la ana a Isiraeli. Pa nthawiyi n’kuti Aisiraeliwo akulira pakhomo la chihema chokumanako.  Koma Pinihasi+ mwana wa Eleazara, mdzukulu wa wansembe Aroni, ataona zimenezi nthawi yomweyo ananyamuka pakati pa khamulo n’kutenga mkondo waung’ono m’dzanja lake.  Iye anathamangira mwamuna wachiisiraeli uja mpaka kukalowa m’hema wake n’kubaya* awiriwo ndi mkondowo. Anabaya mwamuna wachiisiraeli limodzi ndi mkaziyo, mpaka mkondowo unakadutsa kumaliseche kwa mkaziyo. Pamenepo mliri unaleka pakati pa ana a Isiraeli.+  Amene anaphedwa ndi mliriwo analipo 24,000.+ 10  Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: 11  “Pinihasi+ mwana wa Eleazara, mdzukulu wa wansembe Aroni, wabweza mkwiyo wanga+ pa ana a Isiraeli, chifukwa sanalekerere konse zoti anthu azipikisana nane pakati pawo.+ Inetu ndikanawafafanizadi ana a Isiraeliwa, chifukwa ndimafuna kuti azikhala odzipereka kwa ine ndekha basi.+ 12  Pa chifukwa chimenechi, umuuze Pinihasi kuti, ‘Tsopano ndikupangana naye pangano la mtendere. 13  Likhale pangano la unsembe kwa iye ndi mbadwa zake mpaka kalekale,+ chifukwa sanalekerere zoti anthu azipikisana ndi Mulungu wake,+ ndiponso waphimba machimo a ana a Isiraeli.’”+ 14  Dzina la mwamuna wachiisiraeli, amene anaphedwa limodzi ndi mkazi wachimidiyani uja, linali Zimiri mwana wa Salu. Saluyo anali mtsogoleri+ wa nyumba ya makolo a Asimiyoni. 15  Dzina la mkazi wachimidiyani amene anaphedwayo linali Kozibi, mwana wa Zuri.+ Zuri anali mtsogoleri wa fuko la nyumba ina ya makolo ku Midiyani.+ 16  Pambuyo pake Yehova anauza Mose kuti: 17  “Amuna inu, athireni nkhondo Amidiyani, ndipo muwakanthe,+ 18  chifukwa akubweretserani tsoka mochenjera,+ pokukopani kuti muchimwe ku Peori.+ Muwakanthe ndithu, chifukwanso cha zochita za mlongo wawo Kozibi,+ mwana wa mtsogoleri wa ku Midiyani, amene anaphedwa+ pa tsiku limene mliri unakugwerani chifukwa cha zimene zinachitika ku Peori.”+

Mawu a M'munsi

Ena amati “kugwaza.”