Numeri 26:1-65

26  Mliri+ uja utatha, Yehova analankhula ndi Mose ndi Eleazara mwana wa wansembe Aroni, kuti:  “Werengani amuna onse oyenera kupita kunkhondo pakati pa khamu lonse la ana a Isiraeli. Muwerenge kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, potsata nyumba za makolo awo.”+  Chotero Mose ndi wansembe Eleazara+ analankhula ndi Aisiraeliwo m’chipululu cha Mowabu,+ pafupi ndi mtsinje wa Yorodano, kufupi ndi Yeriko,+ kuti:  “Werengani ana onse a Isiraeli kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, monga Yehova analamulira Mose.”+ Tsopano ana onse a Isiraeli amene anatuluka m’dziko la Iguputo ndi awa:  Rubeni anali mwana woyamba kubadwa wa Isiraeli.+ Ana aamuna a Rubeni anali: Hanoki+ amene anali kholo la banja la Ahanoki, Palu+ amene anali kholo la banja la Apalu,  Hezironi+ amene anali kholo la banja la Ahezironi, ndi Karami+ amene anali kholo la banja la Akarami.  Amenewa anali mabanja a Arubeni. Amuna onse owerengedwa m’mabanja awo analipo 43,730.+  Mwana wamwamuna wa Palu anali Eliyabu.  Ana aamuna a Eliyabu anali Nemueli, Datani+ ndi Abiramu.+ Awiriwa, Datani ndi Abiramu, anali osankhidwa a khamulo. Iwowa ndi amene anagwirizana ndi gulu la Kora+ pokangana ndi Mose ndi Aroni, pamene anali kutsutsana ndi Yehova. 10  Zitatero, nthaka inayasama n’kuwameza.+ Koma Kora anafa pamene moto unanyeketsa gulu la amuna 250.+ Choncho iwowa anakhala chitsanzo chopereka chenjezo.+ 11  Koma ana a Kora sanafe.+ 12  Ana aamuna a Simiyoni+ mwa mabanja awo anali awa: Nemueli+ amene anali kholo la banja la Anemueli, Yamini+ amene anali kholo la banja la Ayamini, Yakini+ amene anali kholo la banja la Ayakini, 13  Zera amene anali kholo la banja la Azera, ndi Shauli+ amene anali kholo la banja la Ashauli. 14  Amenewa ndiwo anali mabanja a Asimiyoni. Amuna onse pamodzi analipo 22,200.+ 15  Ana aamuna a Gadi+ ndi mabanja awo anali awa: Zefoni amene anali kholo la banja la Azefoni, Hagi amene anali kholo la banja la Ahagi, Suni amene anali kholo la banja la Asuni, 16  Ozini amene anali kholo la banja la Aozini, Eri amene anali kholo la banja la Aeri, 17  Arodi amene anali kholo la banja la Aarodi, ndi Areli+ amene anali kholo la banja la Aareli. 18  Amenewa ndiwo anali mabanja a ana a Gadi. Amuna onse owerengedwa m’mabanja awo analipo 40,500.+ 19  Ana a Yuda+ anali Ere+ ndi Onani.+ Koma awiriwa anafera m’dziko la Kanani.+ 20  Choncho ana aamuna a Yuda mwa mabanja awo anali awa: Shela+ amene anali kholo la banja la Ashela, Perezi+ amene anali kholo la banja la Aperezi, ndi Zera+ amene anali kholo la banja la Azera. 21  Ana aamuna a Perezi anali Hezironi+ amene anali kholo la banja la Ahezironi, ndi Hamuli+ amene anali kholo la banja la Ahamuli. 22  Amenewa ndiwo anali mabanja a Yuda.+ Amuna onse owerengedwa m’mabanja awo analipo 76,500.+ 23  Ana aamuna a Isakara+ ndi mabanja awo anali awa: Tola+ amene anali kholo la banja la Atola, Puva amene anali kholo la banja la Apuna, 24  Yasubi amene anali kholo la banja la Ayasubi, ndi Simironi+ amene anali kholo la banja la Asimironi. 25  Amenewa ndiwo anali mabanja a Isakara. Amuna onse owerengedwa m’mabanja awo analipo 64,300.+ 26  Ana aamuna a Zebuloni+ anali awa: Seredi amene anali kholo la banja la Aseredi, Eloni amene anali kholo la banja la Aeloni, ndi Yahaleeli+ amene anali kholo la banja la Ayahaleeli. 27  Amenewa ndiwo anali mabanja a Azebuloni. Amuna onse owerengedwa m’mabanja awo analipo 60,500.+ 28  Ana aamuna a Yosefe+ ndi mabanja awo anali Manase ndi Efuraimu.+ 29  Ana aamuna a Manase+ anali Makiri+ amene anali kholo la banja la Amakiri. Makiri anabereka Giliyadi.+ Giliyadi anali kholo la banja la Agiliyadi. 30  Ana aamuna a Giliyadi anali awa: Yezeri+ amene anali kholo la banja la Ayezeri, Heleki amene anali kholo la banja la Aheleki, 31  Asiriyeli amene anali kholo la banja la Aasiriyeli, Sekemu amene anali kholo la banja la Asekemu, 32  Semida+ amene anali kholo la banja la Asemida, ndi Heferi+ amene anali kholo la banja la Aheferi. 33  Koma Tselofekadi, mwana wamwamuna wa Heferi, analibe ana aamuna koma aakazi okhaokha.+ Mayina a ana aakazi a Tselofekadi anali: Mala, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.+ 34  Amenewa ndiwo anali mabanja a Manase. Amuna onse owerengedwa m’mabanja awo analipo 52,700.+ 35  Ana aamuna a Efuraimu+ ndi mabanja awo anali awa: Sutela+ amene anali kholo la banja la Asutela, Bekeri amene anali kholo la banja la Abekeri, ndi Tahani+ amene anali kholo la banja la Atahani. 36  Ana aamuna a Sutela anali Erani amene anali kholo la banja la Aerani. 37  Amenewa ndiwo anali mabanja a ana a Efuraimu.+ Amuna onse owerengedwa m’mabanja awo analipo 32,500. Awa anali ana aamuna a Yosefe ndi mabanja awo.+ 38  Ana aamuna a Benjamini+ ndi mabanja awo anali awa: Bela+ amene anali kholo la banja la Abela, Asibeli+ amene anali kholo la banja la Aasibeli, Ahiramu amene anali kholo la banja la Aahiramu, 39  Sefufamu amene anali kholo la banja la Asefufamu, ndi Hufamu+ amene anali kholo la banja la Ahufamu. 40  Ana aamuna a Bela anali Aridi ndi Namani.+ Aridi anali kholo la banja la Aaridi. Namani anali kholo la banja la Anamani. 41  Amenewa ndiwo anali ana aamuna a Benjamini+ ndi mabanja awo. Amuna onse owerengedwa m’mabanja awo analipo 45,600.+ 42  Ana aamuna a Dani+ mwa mabanja awo anali ochokera kwa Suhamu amene anali kholo la banja la Asuhamu. Awa anali mabanja a Dani+ potsata fuko lawo. 43  Amuna onse owerengedwa m’mabanja onse a Asuhamu analipo 64,400.+ 44  Ana aamuna a Aseri+ ndi mabanja awo anali awa: Imuna+ amene anali kholo la banja la Aimuna, Isivi+ amene anali kholo la banja la Aisivi ndi Beriya amene anali kholo la banja la Aberiya. 45  Ana aamuna a Beriya anali Hiberi amene anali kholo la banja la Ahiberi, ndi Malikieli+ amene anali kholo la banja la Amalikieli. 46  Mwana wamkazi wa Aseri anali Sera.+ 47  Amenewa ndiwo anali mabanja a ana aamuna a Aseri.+ Amuna onse owerengedwa m’mabanja awo analipo 53,400.+ 48  Ana aamuna a Nafitali+ ndi mabanja awo anali awa: Yahazeeli+ amene anali kholo la banja la Ayahazeeli, Guni+ amene anali kholo la banja la Aguni, 49  Yezera+ amene anali kholo la banja la Ayezera, ndi Silemu+ amene anali kholo la banja la Asilemu. 50  Amenewa ndiwo anali mabanja a Nafitali+ potsata fuko lawo. Amuna onse owerengedwa m’mabanja awo analipo 45,400.+ 51  Amenewa ndiwo amuna onse amene anawerengedwa pakati pa ana a Isiraeli. Onse pamodzi analipo 601,730.+ 52  Pambuyo pake, Yehova analankhula ndi Mose kuti: 53  “Anthu amenewa uwagawire dzikoli malinga ndi chiwerengero cha mayinawo, kuti likhale cholowa chawo.+ 54  Amene ali ndi anthu ambiri apatsidwe dziko lalikulu monga cholowa chake, ndipo amene ali ndi anthu ochepa apatsidwe dziko laling’ono monga cholowa chake.+ Aliyense apatsidwe cholowacho malinga ndi chiwerengero cha anthu ake. 55  Njira yokha imene ugawire dzikolo ndiyo mwa kuchita maere basi.+ Onse alandire cholowacho potsata mayina a mafuko a makolo awo. 56  Mtsogoleri wa fuko aliyense um’gawire cholowa chake mwa kuchita maere, amene ali ndi anthu ochuluka kapena anthu ochepa.” 57  Tsopano awa ndi mayina a amuna owerengedwa mwa Alevi+ malinga ndi mabanja awo: Agerisoni, a banja la Gerisoni,+ Akohati, a banja la Kohati,+ ndi Amerari, a banja la Merari.+ 58  Nawa mabanja a Alevi: banja la Alibini,+ banja la Aheburoni,+ banja la Amali,+ banja la Amusi,+ ndi banja la Akora.+ Kohati+ anabereka Amuramu.+ 59  Mkazi wa Amuramu anali Yokebedi,+ mwana wa Levi, amene mkazi wake anam’berekera ku Iguputo. Yokebedi anaberekera Amuramu ana awa: Aroni, Mose ndi mlongo wawo Miriamu.+ 60  Ndiyeno Aroni anabereka Nadabu, Abihu,+ Eleazara ndi Itamara.+ 61  Koma Nadabu ndi Abihu anafa chifukwa chofukiza moto wosaloleka pamaso pa Yehova.+ 62  Onse amene anawerengedwa pakati pa Alevi analipo 23,000. Amenewa anali amuna onse kuyambira amwezi umodzi kupita m’tsogolo.+ Iwowa sanawerengedwe limodzi ndi ana a Isiraeli,+ chifukwa sanafunikire kulandira cholowa pakati pa ana a Isiraeli.+ 63  Awa ndiwo anthu amene Mose ndi wansembe Eleazara anawawerenga pakati pa ana a Isiraeli. Anawawerengera m’chipululu cha Mowabu, pafupi ndi mtsinje wa Yorodano, kufupi ndi Yeriko.+ 64  Koma pakati pa amenewa, panalibe aliyense wa amene anawerengedwa m’chipululu cha Sinai aja, pamene Mose ndi wansembe Aroni anawerenga ana a Isiraeli.+ 65  Zinakhala choncho chifukwa ponena za iwo, Yehova anati: “Mulimonsemo adzafera m’chipululu basi.”+ Choncho, sipanatsale ndi mmodzi yemwe kupatulapo Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni.+

Mawu a M'munsi