Numeri 28:1-31
28 Yehova analankhulanso ndi Mose, kuti:
2 “Lamula ana a Isiraeli kuti, ‘Muzionetsetsa kuti pa nthawi yake yoikidwiratu+ mukupereka kwa ine nsembe yanga, yomwe ndi chakudya changa+ chotentha ndi moto, chotulutsa fungo londikhazika mtima pansi.’+
3 “Uwauze kuti, ‘Muzipereka kwa Yehova nsembe yotentha ndi moto motere: Tsiku lililonse muzipereka nsembe yopsereza ya ana a nkhosa awiri amphongo, achaka chimodzi ndi opanda chilema.+
4 Mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo muzim’pereka nsembe m’mawa. Ndipo mwana wa nkhosa wamphongo winayo, muzim’pereka nsembe madzulo kuli kachisisira.*+
5 Muzipereka nsembezi limodzi ndi ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa,+ monga nsembe yambewu.+ Ufawo muziuthira mafuta oyenga bwino kwambiri okwana gawo limodzi mwa magawo anayi a muyezo wa hini.+
6 Imeneyi ndi nsembe yopsereza+ ya tsiku ndi tsiku imene ndinakulamulani kuphiri la Sinai. Ndinakulamulani kuti muziipereka kwa Yehova monga nsembe yafungo lokhazika mtima pansi, yotentha ndi moto.+
7 Muziipereka pamodzi ndi nsembe yachakumwa+ chokwana gawo limodzi mwa magawo anayi a muyezo wa hini. Pa mwana wa nkhosa wamphongo+ aliyense muzipereka nsembe yachakumwa. Muzithirira Yehova nsembe yachakumwa choledzeretsayo+ m’malo oyera.
8 Mwana wa nkhosa wamphongo winayo muzim’pereka nsembe madzulo kuli kachisisira. Muzim’pereka limodzi ndi nsembe yambewu ndiponso yachakumwa, mofanana ndi nsembe ya m’mawa ija. Izikhala nsembe yotentha ndi moto yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova.+
9 “‘Koma pa tsiku la sabata,+ muzipereka nsembe ana a nkhosa awiri amphongo opanda chilema. Muziwapereka pamodzi ndi ufa wosalala monga nsembe yambewu. Ufawo muziuthira mafuta, ndipo uzikhala wokwana magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa. Muziperekanso nsembe yake yachakumwa.
10 Imeneyi ndi nsembe yopsereza ya tsiku lasabata, yoperekedwa pa tsiku la sabata lililonse. Muziipereka limodzi ndi nsembe yopsereza+ ya tsiku ndi tsiku, pamodzi ndi nsembe yake yachakumwa.+
11 “‘Kumayambiriro kwa mwezi uliwonse, muzipereka nsembe yopsereza kwa Yehova. Nsembeyo izikhala ng’ombe ziwiri zazing’ono zamphongo, nkhosa imodzi yamphongo, ndi ana a nkhosa 7 amphongo opanda chilema. Mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi.+
12 Pang’ombe iliyonse yamphongo, muzipereka ufa wosalala wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa, monga nsembe yake yambewu.+ Ufawo uzikhala wothira mafuta. Nkhosa yamphongo imodziyo+ muziipereka limodzi ndi nsembe yambewu ya ufa wosalala wokwana magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa. Ufawo uzikhala wothira mafuta.
13 Ndipo pa mwana wa nkhosa wamphongo aliyense, yomwe ndi nsembe yopsereza yafungo lokhazika mtima pansi,+ nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova, muziperekanso nsembe yambewu ya ufa wosalala wothira mafuta. Ufawo uzikhala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa.
14 Panyama iliyonse yoperekedwa nsembe muziperekanso nsembe yachakumwa. Ng’ombe yamphongo muziipereka limodzi ndi vinyo wokwana hafu+ ya muyezo wa hini. Nkhosa yamphongo muziipereka limodzi ndi vinyo wokwana gawo limodzi mwa magawo atatu+ a muyezo wa hini. Ndipo mwana wa nkhosa wamphongo muzim’pereka limodzi ndi vinyo wokwana gawo limodzi mwa magawo anayi+ a muyezo wa hini. Zinthu zimenezi muzizipereka monga nsembe yopsereza ya mwezi ndi mwezi, yoperekedwa mwezi uliwonse pa miyezi yonse ya pa chaka.+
15 Muziperekanso mwana wa mbuzi+ monga nsembe yamachimo kwa Yehova, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yachakumwa.+
16 “‘M’mwezi woyamba, pa tsiku la 14, pazikhala pasika wa Yehova.+
17 Ndiyeno pa tsiku la 15 la mwezi umenewu pazikhala chikondwerero. Kwa masiku 7 muzidya mikate yopanda chofufumitsa.+
18 Pa tsiku loyamba la chikondwererocho muzichita msonkhano wopatulika.+ Musamagwire ntchito yolemetsa yamtundu uliwonse pa tsikuli.+
19 Muzipereka nsembe yotentha ndi moto, yomwe ndi nsembe yopsereza+ kwa Yehova. Nsembeyo izikhala ya ng’ombe ziwiri zazing’ono zamphongo, nkhosa imodzi yamphongo, ndi ana a nkhosa 7 amphongo. Mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi.+ Muzionetsetsa kuti nyamazo n’zopanda chilema.+
20 Nsembe zake zambewu+ muzizipereka motere: Ng’ombe yamphongo iliyonse muziipereka limodzi ndi ufa wosalala wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa. Nkhosa yamphongoyo muziipereka limodzi ndi ufa wokwana magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa.+ Ufawo uzikhala wothira mafuta.
21 Pa mwana wa nkhosa wamphongo aliyense pa ana a nkhosa 7 amenewo, muziperekanso ufa wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo+ wa efa.
22 Muziperekanso mbuzi imodzi monga nsembe yamachimo, kuti ikhale yophimbira machimo anu.+
23 Muzipereka nsembe zimenezi, kuwonjezera pa nsembe yopsereza+ ya m’mawa ya tsiku ndi tsiku.+
24 Mofanana ndi zimenezi, muziperekanso nsembe yotentha ndi moto tsiku lililonse kwa masiku 7, monga chakudya+ cha Yehova, monganso nsembe yafungo lokhazika mtima pansi kwa iye.+ Muziipereka limodzi ndi nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, ndi nsembe yake yachakumwa.
25 Pa tsiku la 7 muzikhala ndi msonkhano wopatulika.+ Musamagwire ntchito yolemetsa yamtundu uliwonse pa tsikuli.+
26 “‘Ndipo pa tsiku la zipatso zoyambirira,+ pamene muzipereka nsembe yambewu zatsopano kwa Yehova, paphwando lanu la masabata,+ muzichita msonkhano wopatulika. Musamagwire ntchito yolemetsa yamtundu uliwonse pa tsikuli.+
27 Muzipereka nsembe yopsereza yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova. Nsembeyo izikhala ya ng’ombe ziwiri zazing’ono zamphongo, nkhosa imodzi yamphongo, ndi ana a nkhosa 7 amphongo, achaka chimodzi.+
28 Muziperekanso nsembe yake yambewu ya ufa wosalala wothira mafuta. Ufawo uzikhala wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa pa ng’ombe yamphongo iliyonse. Pankhosa yamphongo imodziyo, muzipereka ufa wokwana magawo awiri mwa magawo 10+ a muyezo wa efa.
29 Pa aliyense wa ana a nkhosa amphongo 7 amenewo, muzipereka ufa wokwana gawo limodzi mwa magawo 10+ a muyezo wa efa.
30 Komanso muzipereka mwana wa mbuzi wophimbira machimo anu.+
31 Muzipereka zimenezi+ kuwonjezera pa nsembe yanu yopsereza ya tsiku ndi tsiku ndi nsembe yake yambewu. Muzionetsetsa kuti nyamazo n’zopanda chilema.+ Muziperekanso nsembe yake yachakumwa.+