Numeri 29:1-40
29 “‘Pa tsiku loyamba la mwezi wa 7, muzichita msonkhano wopatulika.+ Musamagwire ntchito yolemetsa yamtundu uliwonse.+ Lizikhala tsiku lanu loliza lipenga.+
2 Pa tsikuli muzipereka nsembe yopsereza yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova. Nsembeyo izikhala ya ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo, ndi ana a nkhosa amphongo 7, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, wopanda chilema.+
3 Muziperekanso ufa wosalala wothira mafuta monga nsembe zake zambewu. Ufawo uzikhala wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa pang’ombe yamphongoyo, magawo awiri mwa magawo 10 pankhosa yamphongoyo,+
4 ndi gawo limodzi mwa magawo 10 pa aliyense wa ana a nkhosa amphongo 7+ amenewo.
5 Muziperekanso mwana wa mbuzi mmodzi wamphongo, monga nsembe yamachimo yophimbira machimo anu.+
6 Muzipereka nsembe zimenezi kuwonjezera pa nsembe yopsereza+ ya mwezi ndi mwezi, limodzi ndi nsembe yake yambewu.+ Muzizipereka kuwonjezeranso pa nsembe yopsereza+ ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu,+ limodzinso ndi nsembe zachakumwa.+ Muzipereka nsembe zopserezazo malinga ndi dongosolo lake la nthawi zonse, monga nsembe zotentha ndi moto zopereka fungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova.+
7 “‘Pa tsiku la 10 la mwezi wa 7 umenewu, muzichita msonkhano wopatulika,+ ndipo muzidzisautsa.*+ Musamagwire ntchito yamtundu uliwonse.+
8 Pa tsikuli muzipereka nsembe yopsereza yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova. Nsembeyo izikhala ya ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, ndi ana a nkhosa 7 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi.+ Muzionetsetsa kuti nyamazo n’zopanda chilema.+
9 Muziperekanso nsembe zake zambewu za ufa wosalala wothira mafuta. Popereka ng’ombe yamphongoyo muziperekanso ufa wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa. Popereka nkhosa yamphongoyo+ muziperekanso ufa wokwana magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa.
10 Popereka aliyense wa ana a nkhosa 7 amphongowo,+ muziperekanso ufa wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa.
11 Muziperekanso mwana wa mbuzi mmodzi monga nsembe yamachimo.+ Muzim’pereka kuwonjezera pa nsembe yamachimo pa tsiku lophimba machimo, ndi nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe zake zambewu ndiponso zachakumwa.+
12 “‘Pa tsiku la 15 la mwezi wa 7,+ muzichita msonkhano wopatulika.+ Musamagwire ntchito yolemetsa yamtundu uliwonse.+ Muzichita chikondwerero kwa Yehova masiku 7.+
13 Pa tsiku limeneli muzipereka nsembe yopsereza+ yotentha ndi moto yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova. Nsembe imeneyo izikhala ya ng’ombe 13 zazing’ono zamphongo, nkhosa zamphongo ziwiri, ndi ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi. Muzionetsetsa kuti nyamazi n’zopanda chilema.+
14 Muziperekanso nsembe zake zambewu za ufa wosalala wothira mafuta. Iliyonse ya ng’ombe 13 zamphongozo muziiperekera ufa wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa. Iliyonse ya nkhosa zamphongo ziwirizo muziiperekera ufa wokwana magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa.+
15 Aliyense wa ana a nkhosa 14 amphongowo, muzim’perekera ufa wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa.+
16 Muziperekanso mwana wa mbuzi mmodzi monga nsembe yamachimo, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu ndiponso nsembe yake yachakumwa.+
17 “‘Pa tsiku lachiwiri, muzipereka ng’ombe 12 zazing’ono zamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo, ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, wopanda chilema.+
18 Popereka nyama zimenezi, ng’ombe zamphongo, nkhosa zamphongo, ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu+ ndi nsembe zake zachakumwa,+ malinga ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse.+
19 Muziperekanso mwana wa mbuzi mmodzi monga nsembe yamachimo.+ Muzim’pereka kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku ndi nsembe yake yambewu, limodzi ndi nsembe zake zachakumwa.+
20 “‘Pa tsiku lachitatu, muzipereka ng’ombe 11 zamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo ndi ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, wopanda chilema.+
21 Popereka nyama zimenezi, ng’ombe zamphongo, nkhosa zamphongo, ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu+ ndi nsembe zake zachakumwa,+ malinga ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse.
22 Muziperekanso mbuzi imodzi monga nsembe yamachimo,+ kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu, ndiponso nsembe yake yachakumwa.
23 “‘Pa tsiku lachinayi, muzipereka ng’ombe 10 zamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo, ndi ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, wopanda chilema.+
24 Popereka nyama zimenezi, ng’ombe zamphongo, nkhosa zamphongo, ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu+ ndi nsembe zake zachakumwa,+ malinga ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse.+
25 Muziperekanso mwana wa mbuzi mmodzi monga nsembe yamachimo,+ kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku,+ limodzi ndi nsembe yake yambewu, ndiponso nsembe yake yachakumwa.+
26 “‘Pa tsiku lachisanu, muzipereka ng’ombe 9 zamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo, ndi ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, wopanda chilema.+
27 Popereka nyama zimenezi, ng’ombe zamphongo, nkhosa zamphongo, ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu+ ndi nsembe zake zachakumwa,+ malinga ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse.+
28 Muziperekanso mbuzi imodzi monga nsembe yamachimo,+ kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu, ndiponso nsembe yake yachakumwa.+
29 “‘Pa tsiku la 6, muzipereka ng’ombe 8 zamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo, ndi ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, wopanda chilema.+
30 Popereka nyama zimenezi, ng’ombe zamphongo, nkhosa zamphongo, ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu+ ndi nsembe zake zachakumwa,+ malinga ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse.+
31 Muziperekanso mbuzi imodzi monga nsembe yamachimo,+ kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu, ndiponso nsembe yake yachakumwa.+
32 “‘Pa tsiku la 7, muzipereka ng’ombe 7 zamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo, ndi ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, wopanda chilema.+
33 Popereka nyama zimenezi, ng’ombe zamphongo, nkhosa zamphongo, ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu+ ndi nsembe zake zachakumwa,+ malinga ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse la zimenezi.+
34 Muziperekanso mbuzi imodzi monga nsembe yamachimo,+ kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu, ndiponso nsembe yake yachakumwa.+
35 “‘Pa tsiku la 8, muzichita msonkhano wapadera.+ Musamagwire ntchito yolemetsa yamtundu uliwonse.+
36 Pa tsikuli, muzipereka nsembe yopsereza yotentha ndi moto yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova. Nsembeyo izikhala ya ng’ombe imodzi yamphongo, nkhosa imodzi yamphongo, ndi ana a nkhosa 7 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, wopanda chilema.+
37 Popereka nyama zimenezi, ng’ombe yamphongo, nkhosa yamphongo, ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu+ ndi nsembe zake zachakumwa,+ malinga ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse.+
38 Muziperekanso mbuzi imodzi monga nsembe yamachimo,+ kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu, ndiponso nsembe yake yachakumwa.+
39 “‘Muzipereka zimenezi kwa Yehova pa zikondwerero zanu.+ Muzizipereka kuwonjezera pa zopereka zanu zalonjezo,+ ndi nsembe zanu zaufulu+ zimene mumapereka monga nsembe zanu zopsereza,+ nsembe zanu zambewu,+ nsembe zanu zachakumwa,+ ndi nsembe zanu zachiyanjano.’”+
40 Pamenepo Mose anauza ana a Isiraeli zonse monga mmene Yehova anamulamulira.+
Mawu a M'munsi
^ “Kudzisautsa” pano kungatanthauze kusala chakudya ndiponso kutsatira malamulo ena ofanana ndi kuchita zimenezi.